Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Wotsogoza
1 Kukhala woyang’anira mumpingo ndi ntchito yaikulu. (Mac. 20:28; 1 Tim. 3:1) Iyi ndi nkhani yoyamba mwa nkhani zimene zidzalongosola ntchito zosiyanasiyana za akulu achikristu kotero kuti tonsefe tidziŵe bwino ntchito yofunika imene iwo amatichitira.
2 Sosaite imaika woyang’anira wotsogoza kuti atumikire kwa nthaŵi yosadziŵika. Pamene woyang’anira wotsogoza agwirizanitsa zinthu, zimathandiza akulu ena kusamalira bwino maudindo amene anapatsidwa. (Uminisitala Wathu, tsamba 42) Kodi zimenezi zimaphatikizaponji?
3 Woyang’anira wotsogoza amalandira makalata a mpingo ndipo mwamsanga amawapereka kwa mlembi kuti awasamalire. Pokonzekera msonkhano wa akulu, woyang’anira wotsogoza amalandira malingaliro a akulu ena pankhani zoti akakambitsirane ndi kukonza ajenda yake. Amakhalanso tcheyamani wamsonkhano wa akulu. Pamene asankha zochita, amaonetsetsa kuti zikuchitidwadi moyenerera. Amayang’anira kukonzekera Msonkhano Wautumiki ndi kukonza ndandanda ya okamba nkhani zapoyera. Amavomereza zilengezo zonse za pampingo, kulipiridwa kwa zoonongedwa zonse zoyenerera, ndipo amaonetsetsa kuti maakaunti ampingo akuŵerengedwa pakutha pa miyezi itatu iliyonse.
4 Monga tcheyamani, woyang’anira wotsogoza amagwirizanitsa ntchito ya Komiti Yautumiki ya Mpingo. Pamene wophunzira Baibulo apempha kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa kapena pamene wofalitsa wosabatizidwa akufuna kubatizidwa, woyang’anira wotsogoza amalinganiza kuti akulu akumane naye. Woyang’anira wotsogoza amatsogoleranso pokonzekera kuchezera kwa woyang’anira dera kotero kuti mpingo upindule mokwanira ndi mlungu wapaderawo.
5 Zochita za woyang’anira wotsogoza nzochuluka ndi zosiyanasiyana. Pamene asamalira mathayo ake modzichepetsa ndi ‘mwachangu,’ tonsefe tingachite mbali yathu mwa kugwirizana ndi akulu. (Aroma 12:8) Ngati ‘timvera’ ndi ‘kugonjera’ amene amatitsogolera, iwo adzachita ntchito yawo ndi chimwemwe chokulirapo.—Aheb. 13:17.