Limbikitsanani mwa Kuyankha Pamisonkhano
1 Pa Ahebri 10:24 tikulimbikitsidwa ‘kufulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ Izi zimaphatikizapo kulimbikitsana mwa kuyankha zomveka pamisonkhano ya mpingo. Nchifukwa chiyani tifunikira kuyankha? Kodi tingayankhe bwanji? Kodi ndani amene amapindula?
2 Taganizirani za nthaŵi zochulukazo zimene mumapindula pomvetsera ena akupereka ndemanga zachidule, zomveka zimene zimakuthandizani kumvetsetsa ndi kukulimbikitsani mwauzimu. Muli ndi mwayi wowachitiranso zofananazo. Pamene mutengamo mbali, mumasonyeza chikhumbo chanu cha ‘kugaŵira mtulo wina wauzimu’ kuti mulimbikitse onse amene alipo.—Aroma 1:11, 12.
3 Mmene Mungaperekere Mayankho Abwino: Musapereke yankho lalitali, mukumatchula mfundo iliyonse ya ndimeyo. Ndemanga zitalizitali nthaŵi zambiri sizisonyeza yankho lenileni ndipo zingachititse ena ulesi kuti ayankheko. Yankho loyambirira pandime liyenera kukhala lachidule, logwirizana ndi funso losindikizidwalo. Ndiyeno amene akupereka ndemanga zina angasonyeze mmene nkhaniyo ingagwiritsiridwe ntchito kapena angasonyeze mmene malemba akugwirira ntchito. Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 90-2.
4 Ngati kuyankha pamisonkhano kumakuchititsani mantha, konzeranitu ndemanga yachidule pasadakhale, ndi kupempha wochititsa kuti akakutchuleni pandime imeneyo. Mutachita zimenezi pamisonkhano ingapo, sikudzakhala kovuta kumatengamo mbali. Kumbukirani kuti Mose ndi Yeremiya anati analibe chidaliro chakuti angalankhule pagulu. (Eks. 4:10; Yer. 1:6, NW, mawu a mtsinde.) Koma Yehova anawathandiza kuti amyankhulire, ndipo adzakuthandizaninso.
5 Kodi Ndani Amene Adzapindula ndi Mayankho Anu? Inu mwini mumapindula chifukwa mayankho anu amakhomereza zolimba choonadi m’maganizo ndi m’mtima mwanu, kupangitsa kukhala kosavuta kwa inu kukumbukira nkhaniyo panthaŵi ina. Ndiponso, ena amapindula pakumva ndemanga zanu zolimbikitsa. Timalimbikitsidwa pamene aliyense, kaya ndi wozoloŵera, mwana, wamanyazi, kapena wachatsopano, akuyesayesa kulengeza chikhulupiriro chake pamisonkhano ya mpingo.
6 Tidzaonadi kuti ‘mawu a pa nthaŵi yake ali abwino’ pamene agwiritsidwa ntchito kulimbikitsa ena pamisonkhano!—Miy. 15:23.