Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/98 tsamba 1
  • Tiyenera Kuwafikira Mobwerezabwereza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tiyenera Kuwafikira Mobwerezabwereza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani Kulalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Tafola Gawo Lathu Kambirimbiri!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Kodi Nchifukwa Ninji Timabwererako?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Musaleme Pakuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 12/98 tsamba 1

Tiyenera Kuwafikira Mobwerezabwereza

1 Kodi panthaŵi yoyamba imene munthu wina analankhula nanu za uthenga wabwino munavomereza? Ngati simunatero, muyenera kuti mukuyamikira kuti Mboni za Yehova zinakufikirani mobwerezabwereza mpaka mutavomera kuphunzira Baibulo. Nkwabwino kulingalira zimenezi pamene mukugwira ntchito mobwerezabwereza m’gawo lanu.

2 Miyoyo ya anthu ikusintha nthaŵi zonse. Akukumana ndi mavuto kapena mikhalidwe yatsopano, akumva nkhani zoipa m’dera lawo kapena m’dzikoli, akukumana ndi mavuto a zachuma, kapena ena a pabanja akudwala mwina kumwalira. Zinthu zoterezi zingawachititse kufuna kudziŵa chifukwa chake pali mavuto oterewa. Tiyenera kuzindikira zinthu zimene zikuvutitsa anthu maganizo ndiyeno nkuwatonthoza.

3 Iyi ndi Ntchito Yopulumutsa Anthu: Taganizirani za antchito opulumutsa anthu pamalo pomwe pachitika ngozi. Ngakhale kuti ena angamafufuze m’malo mmene mukupezeka opulumuka ochepa, sagwa ulesi nkusiya chifukwa chakuti antchito anzawo akupeza opulumuka ochuluka mbali ina. Ntchito yathu yopulumutsa anthu sinathebe. Chaka chilichonse, timapeza anthu zikwi mazanamazana amene akufuna kupulumuka “chisautso chachikulu.”—Chiv. 7:9, 14.

4 “Aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.” (Aroma 10:13-15) Mawu amenewa ayenera kukhomereza mwa aliyense wa ife kufunika kolimbikira kulalikira. Kuchokera pamene gawo lathu linayamba kufoledwa, ana akula ndipo tsopano ndi anthu akuluakulu otha kulingalira za tsogolo lawo ndi chifuno cha moyo. Tilibe njira yodziŵira kuti ndani amene adzamvetsera potsirizira pake. (Mlal. 11:6) Ambiri amene kale anali kutsutsa avomereza choonadi. Ntchito yathu si kuweruza anthu, koma kuwapatsabe mwayi womva uthenga ndi kupulumutsidwa ku dziko lakaleli. Monga anachitira ophunzira a Yesu oyambirira, tiyenera ‘kupitabe’ komwe kuli anthu ndi kuyesa kudzutsa chikondwerero chawo mu uthenga wa Ufumu.—Mat. 10:6, 7.

5 Kukhalabe kwathu ndi mwayi wolalikira kukusonyeza chifundo cha Yehova. (2 Pet. 3:9) Pamene tilola anthu ena kuti azimva uthenga mobwerezabwereza, timazindikiritsa chikondi cha Mulungu, ndipo mwa njirayi timamtamanda.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena