Lalikirani Uthenga Wabwino Mofunitsitsa
1 “Ndilakalaka kuonana ndinu . . . Ndilikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso.” Ndi mmene mtumwi Paulo anafotokozera malingaliro ake kumayambiriro kwa kalata yake yopita kwa abale a ku Roma. N’chifukwa chiyani Paulo anali kufunitsitsa kuonana nawo? Iye anati: “Kuti ndikaone zobala zina mwa inunso . . . Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa.”—Aroma 1:11-16.
2 Paulo anasonyeza kufunitsitsa kofananako polankhula ndi amuna akulu a ku Efeso. Iye anawakumbutsa kuti: “Kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya . . . , sindinakubisirani . . . kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba, ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene.” (Mac. 20:18-21) M’magawo ake onse, Paulo anali ndi cholinga chofalitsa uthenga wabwino wachipulumutso ndi kupeza zipatso za Ufumu. Ndi chitsanzodi chabwino kwambiri choti titsatire!
3 Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimasonyeza kufunitsitsa kofananako polengeza uthenga wabwino m’dera lathu? M’malo moona ntchito yolalikira monga ntchito wamba, kodi ndili wofunitsitsa kuuza anthu ochuluka mmene ndingathere za uthenga wabwino? Kodi ndalingalira mwapemphero mikhalidwe yanga? Kodi ndayesera njira zonse zolalikirira m’dera lathu, monga kulalikira kukhomo ndi khomo, pamakwalala, m’malo a ntchito, patelefoni, ndi mwamwayi?’
4 Tenganimo Mbali Mofunitsitsa m’April: Mwezi wa April ndi nthaŵi yabwino yowonjezera mbali yathu muntchito yolalikira. Kuchepetsedwa kwa maola ofunika kuyenera kuchititsa anthu ambiri kulembetsa upainiya wothandiza. Mwina mikhalidwe yanu ingakuloleni kutumikira monga mpainiya wothandiza m’April ndi m’May. Kapena mukhoza kulembetsa upainiya wokhazikika, popeza maola ofunika kwa mpainiya wokhazikika achepetsedwa. Ngati ndinu wofalitsa mumpingo, kodi mungathere nthaŵi yochuluka koposa kale mu utumiki wakumunda m’mwezi uno ndi wamaŵa, kuthandiza awo amene ali okhoza kuchita upainiya? Zimenezo zidzasangalatsa mtima wa Yehova!
5 Ofalitsa Ufumu onse ayenera kupitiriza kusonyeza kufunitsitsa mwa kuchita khama m’ntchito yolalikira mofanana ndi Paulo. Kuchita zonse zimene tingathe mu utumiki kudzatipatsa chimwemwe chenicheni. Paulo anapeza chimwemwe chimenechi mu utumiki wake wopatulika. Tidzachita bwino kutsatira chitsanzo chake chabwino kwambiri.—Aroma 11:13; 1 Akor. 4:16.