Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu”
1 Pamene Aisrayeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawalimbikitsa kuti aziyamikira malangizo a Mulungu. Anawauza kuti: “Sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.” (Deut. 32:45-47) Kodi sitiyamika Yehova kuti miyoyo yathu ndi yamtengo wapatali kwa iye ndi kuti akupitirizabe kutitsogoza kudzera m’Mawu ake amtengo wapataliwo? Chotero tikuyembekezera mwachidwi Msonkhano Wachigawo wa masiku atatu wa “Mawu Aulosi a Mulungu” ndi zimene Yehova watikonzera.
2 Chaka chino, misonkhano yachigawo yakonzedwa bwino m’madera 15 m’Malaŵi monse muno. Pologalamu yamsonkhano idzachitika mu Chicheŵa, Chingelezi ndi Chitumbuka.
3 Mosakayikira mwakonza kale zokapezekapo tsiku lililonse la msonkhanowu chifukwa mukudziŵa kuti Yehova amayembekezera inu kupezekapo. Dziŵani kuti Yehova amaona zoyesayesa za aliyense komanso kudzimana kumene atumiki ake amapanga ndi cholinga chokapezekapo, ndipo amakumbukira amene amasonyeza kuyamikira. (Aheb. 6:10) Mwa kupezekapo tsiku lililonse lamsonkhano kuyambira pa nyimbo yotsegulira mpaka pemphero lomaliza, timasonyeza kwa Yehova kuti timaona mawu ake kukhala amtengo wapatali. (Deut. 4:10) Timasonyezanso kuyamikira ntchito yaikulu imene abale athu ambiri amagwira polinganiza msonkhano.
4 Kulinganiza kuti anthu a Mulungu zikwizikwi asonkhane pamsonkhano umodzi kumafuna kukonzekera komanso dongosolo labwino. Kudziŵa kuti makonzedwe a msonkhano akonzedwa mwachikondi kaamba ka ife kumatisonkhezera kugwirizana, kuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.” (1 Akor. 14:40) Chidziŵitso ndi zikumbutso zotsatirazi zaperekedwa kuti mukafike pamsonkhano mutakonzekera bwino kuti mukasangalale ndi chakudya chauzimu komanso mayanjano achikristu.
Msonkhano Usanachitike
5 Kodi amene mumachita nawo phunziro la Baibulo ndi anthu ena okondwerera akufunika thandizo popanga makonzedwe awo okapezeka kumsonkhano? Zimene adzaona ndi kumva zingawasonkhezere kukhala alambiri a Yehova. (1 Akor. 14:25) Akulu ayenera kuona aliyense amene akufunikira thandizo la malo ogona kapena kayendedwe, makamaka anthu achikulire mumpingo, ndipo mwachikondi aonetsetse kuti zosoŵa zawo zasamaliridwa.—Agal. 6:10.
6 Popeza Dipatimenti ya Chipatala pamsonkhano ilipo kaamba ka zochitika za mwadzidzidzi zokha, ndi bwino popita kumsonkhano kunyamula mankhwala anu monga asipulini, zomangira mabala, mankhwala ochita kukwemba, mankhwala a m’mimba, ndi zina zoterozo ngati mukukhulupirira kuti mukazifuna. Ngati inu kapena wokondedwa wanu ali ndi matenda oopsa monga a mtima, nthenda ya shuga, kapena amakomoka, chonde nyamulani mankhwala ofunikira popita kumsonkhano. Kukakhala kwanzeru kuti wapabanja kapena bwenzi lake amene akudziŵa bwino za vutolo akhale naye pafupi nthaŵi zonse, popeza amenewa ndiye angathe kupereka thandizo loyenera.
7 Popita kumsonkhano ndi pobwerako, mosakayikira padzapezeka mipata yochitira umboni wamwamwayi. Kodi mudzakhala okonzeka kugaŵira ena choonadi? Tonsefe, kuphatikizapo ana aang’ono, tingatengemo mbali mwa kugaŵira mathirakiti kwa ogulitsa petulo, adalaivala a mabasi, ndi enanso amene tingakumane nawo paulendo wathu. Pakapezeka mipata yoti mukhoza kugaŵira magazini, mabolosha, kapena mabuku ena kwa anthu okondwerera. Khalani okonzeka kuchita umboni wamwamwayi kwa anthu amene mwina simungawafikire ndi ulaliki wanthaŵi zonse.
Pamsonkhano
8 Abale ndi alongo okalamba adzawasungira malo abwino, ndipo malo ena adzakhala a anthu opunduka ndi apanjinga za opunduka. Tsiku lililonse pamene mukuchoka pamalo panu, onetsetsani kuti muli ndi katundu wanu yense.
9 Kuti tisonkhane m’chiŵerengero chochuluka pamisonkhano yathu yachigawo, timafunikira kumvera malamulo a m’deralo, malamulo onena za moto, ndi mfundo zina za chitetezo. Choncho, njira zapakati pa mizere ya mipando ziyenera kukhala zopanda kanthu kuti anthu azitha kuyenda mosavuta.
10 Kodi mudzabatizidwa pamsonkhano wachigawo? Papologalamu ya Loŵeruka m’maŵa, gawo lina la mipando lidzakhala la anthu opita ku ubatizo, ndipo akalinde adzakusonyezani malo amenewa. Ngati n’kotheka, chonde khalani pamalo amenewa mapologalamu asanayambe. Mudzatenge Baibulo, nyimbo, thaulo ndi zovala zanu zoloŵera m’madzi zaulemu. Masikipa olembalemba, ndi zovala zofanana nazo sizoyenera pachochitika cholemekezeka chimenechi. Akulu popenda mafunso a m’buku la Uminisitala Wathu ndi anthu opita ku ubatizo, atsimikize kuti aliyense akumvetsa mfundozi. Popeza kuti ubatizo ndi chizindikiro cha kudzipatulira kwa munthuwe pawekha kwa Yehova Mulungu, sikoyenera kuti amene akubatizidwa agwirane manja pobatizidwa.
11 Makamera, mavidiyokamera, ndi mawailesi akaseti zingagwiritsidwe ntchito pamsonkhano. Komabe, malo amene mwaziika kapena pozigwiritsa ntchito musatseke nazo njira, kutchingira ena, kapena kudodometsa nazo ena kumvetsera pologalamu. Ziyenera kukhala ndi zonse zofunika; kutanthauza kuti zisalumikizidwe kumagetsi kapena kuzokuzira mawu.
12 Popeza matelefoni oyenda nawo komanso tizipangizo tolira tolandirira uthenga zikuwonjezereka, chonde samalani kuti zinthu zimenezi sizikukudodometsani kumvetsera pologalamu kapenanso awo amene mwakhala nawo pafupi. Telefoni iliyonse yokhudza zangozi iyenera kuimbidwa ndi awo amene apatsidwa chilolezo ndi oyang’anira msonkhanowo, osati aliyense payekha mogwiritsa ntchito telefoni yake. Ngati pabuka vuto lamwadzidzidzi, mwamsanga uzani kalinde m’gawo lanulo. Akalinde anaphunzitsidwa mmene ayenera kuchitira pakabuka vuto lamwadzidzidzi.
13 Kaamba ka nthaŵi ndi kupeputsa zinthu, Sosaite imatipempha kunyamula zakudya zathu za masana za tsiku lililonse la msonkhano. Abale ambiri atsatira malangizo amenewa ndipo apeza kuti akauzidwa kupita kokapuma masana, amatha kukhala pansi ndi mabanja awo ndi kudya chakudya chimene abwera nacho tsiku limenelo. Anena kuti nthaŵi yopuma yamasana komanso nthaŵi yowonjezereka yokhala pamodzi ndi abale komanso alongo awo yakhala yosangalatsa. Izi zimafuna kuguliratu zakudya. Tikupempha kuti onse opezekapo atsatire malangizo amenewa. Anthu okondwerera amene adzapite nanu kumsonkhano ayeneranso kubweretsa zakudya zawo. Chonde samalani kwambiri pamene mukugwiritsa ntchito zotengera zagalasi. Moŵa suloledwa pamalo a misonkhano.
14 Kodi mungadzipereke kukathandiza kuyeretsa malo a msonkhano pamapeto a mapologalamu tsiku lililonse? Kapena kodi mungagwire ntchito mu imodzi mwa madipatimenti ena apamsonkhano? Ngati mungathandize, fikani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhanopo. Ana osafika zaka 16 zakubadwa akhoza kuthandiza mwa kugwira ntchito pamodzi ndi kholo kapena wachikulire wina. Ndiponso, aliyense angathandize kuyeretsa malo mwa kuonetsetsa kuti zinyalala zonse zatoledwa ndi kutayidwa m’malo oyenera.
15 Talandira malangizo abwino kwambiri a kavalidwe ndi kapesedwe koyenera pamisonkhano yathu. Mwachitsanzo: Tili ndi malangizo a nkhani imeneyi m’mphatika za Utumiki Wathu wa Ufumu, tili ndi zitsanzo ndi zithunzi m’mabuku athu, ndipo chachikulu koposa, tili ndi zimene Yehova akunena m’Baibulo. (Aroma 12:2; 1 Tim. 2:9, 10) Anthu amatidziŵa ndipo amadziŵa chifukwa chake tasonkhana m’mzinda wawowo. Choncho, kavalidwe ndi kapesedwe kathu ndi umboni wamphamvu paokha. Anthu a Yehova ambiri amapereka chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Komabe, nthaŵi zina, timaona mzimu wa dzikoli ukuoneka pakavalidwe ndi pakapesedwe mwa anthu ena ofika pamisonkhano yathu. Mtundu uliwonse wa zovala zoonekera mkati umakayikitsa ngati munthuyo alidi wauzimu. Maonekedwe aulemu komanso audongo ndiwo ali ofunika kwambiri. Chotero, mitu ya mabanja iyenera kuonetsetsa zimene am’banja lawo akuvala. Izi zimagwiranso ntchito pamene sitili pamalo a msonkhano. Kuvala mabaji athu popita ndi pobwera, tikatha mapologalamu a tsiku lililonse kumatigwirizanitsa ife ndi Yehova komanso anthu ake oyera.—Yerekezerani ndi Marko 8:38.
16 Mfumu yanzeru Solomo inauziridwa kulemba kuti “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana” ndi kutinso “mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” (Miy. 22:15; 29:15) Pamapologalamu, Mboni zachinyamata zosayang’aniridwa zasokoneza abale ndi alongo ofuna kupindula ndi pologalamu. N’kwachidziŵikire kuti ana amenewa sapindula ndi pologalamu yauzimu imene imakonzedwa mowalingaliranso. Popeza makolo ndiwo ali ndi mlandu kwa Yehova kaamba ka khalidwe la ana awo, amayi kapena atate angadziŵe kuti ana ali akhalidwe labwino ndipo akumvetsera malangizo a Yehova kokha ngati akhala nawo pamodzi. Akalinde adzalankhula ndi munthu aliyense woyambitsa chisokonezo ndipo adzawapempha kuti aleke kuchita zimenezo, ndipo mwachikondi adzawakumbutsa kuti azimvetsera pologalamu.
17 Chifukwa timaitana anthu osiyanasiyana pamisonkhano yathu, ndi kwanzeru kusamalira ana ndi katundu wathu. Ana athu ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. Koma timadziŵa kuti dzikoli limasonyeza khalidwe la Satana ladyera. Choncho, chonde dziŵani kumene ana anu ali nthaŵi zonse. Komanso, nthaŵi zonse makamera, zikwama zoikamo ndalama, ndi zinthu zina zamtengo wapatali ziyenera kukhala nanu ndipo musazisiye pampando wanu. Tsimikizani kuti galimoto lanu ndi lokiya, ndipo ikani katundu wanu kubuti kapena m’tengeni. Izi zimachepetsa chikoka chakuti munthu athyole galimoto lanulo.
18 N’kolimbikitsa kuona abale ndi alongo akulemba notsi mapologalamu a msonkhano ali mkati. Notsi zachidule zidzakuthandizani kumvetsera kwambiri ndi kukukumbutsani mfundo zazikulu. Kupenda notsi zanu nthaŵi ina ndi banja lanu kapena ndi anzanu kumakupangitsani inu kulingalira mfundo zazikulu za msonkhanowo kotero kuti musaziiŵale.
19 Nthaŵi zonse anthu a Yehova akhala akupereka moolowa manja kuchirikiza zinthu zateokalase. (Eks. 36:5-7; 2 Mbiri 31:10; Aroma 15:26, 27) Zopereka zanu zodzifunira za ntchito yapadziko lonse zimagwira ntchito yolipirira zinthu monga malo aakulu amene kumachitikira misonkhano. Ngati zopereka zanu zili cheke, chonde lembani kuti ilipidwe ku “Watchtower.”
20 Monga momwe zinalembedwera pa Amosi 3:7, Yehova anati “sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” Monga “Wakuvumbulutsa zinsinsi,” Yehova analemba m’Baibulo maulosi ambiri zedi amene akwaniritsidwa ndendende. (Dan. 2:28, 47) Malonjezo aakulu adzakwaniritsidwa posachedwapa. Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu” idzalimbitsa chikhulupiriro chanu m’malonjezo a Mulungu. Dzamvetsereni mosamalitsa mawu amene Yehova adzakuuzani. Gwiritsani ntchito zimene mudzaona ndi kumva—mu utumiki, mumpingo, ndi m’moyo wanu. Tikupempherera madalitso ochuluka a Yehova pa makonzedwe anu onse okapezeka tsiku lililonse paphwando lalikulu lauzimu limeneli!
[Bokosi patsamba 6]
Zikumbutso za Msonkhano
Khalidwe Labwino: N’kofunika kwambiri kuti onse ofika pamsonkhano akhale akhalidwe labwino, akumaona mwaulemu malo a msonkhano monga “nyumba ya Mulungu.” (Sal. 55:14) Pankhani, seŵero, nyimbo, ndipo makamaka papemphero, chonde peŵani kuchita kalikonse kamene kangadodometse ena amene akumvetsera pologalamu. Kuyendayenda kosafunikira, kulankhulana, kapena kugwiritsira ntchito makamera afulashi kapena mavidiyo lekoda mwanjira imene imadodometsa awo amene akuyesa kumvetsera kwambiri zimene zikunenedwa kukakhala kupanda ulemu. Kuganizira ena ndi khalidwe lathu labwino zidzasonyeza kuti tikuyamikira ndi mtima wonse maphunziro aumulungu ndipo tabwera ku msonkhano kudzalangizidwa ndi Yehova.
Misonkhano ya Utumiki wa pa Beteli ndi Sukulu Yophunzitsa Utumiki: Pamsokhano padzakhala msonkhano wa akulu osakwatira kapenanso atumiki otumikira osakwatira azaka zoyambira 23 mpaka 50 amenenso ali apainiya amene akufuna kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki kaamba ka maphunziro amenewo. Padzakhalanso msonkhano wa ofalitsa aliyense amene ali ndi zaka 19 mpaka 35 zakubadwa amene ali nzika za dziko lino ndipo akufuna kuloŵa mu utumiki wa pa Beteli. Malo ndi nthaŵi ya misonkhano imeneyi idzalengezedweratu. Onani tsatanetsatane wa misonkhanoyi pa pologalamu ya msonkhano.
Ubatizo: Loŵeruka m’maŵa opita ku ubatizo ayenera kukhala pamalo amene awakonzera mapologalamu asanayambe. Aliyense wopita ku ubatizo ayenera kubwera ndi chovala choloŵera m’madzi chaulemu ndi thaulo. Wokamba nkhani akatha kukamba nkhani yaubatizo ndi pemphero, tcheyamani wa mbaliyo adzapereka malangizo achidule kwa opita ku ubatizo kenako adzaitanitsa nyimbo. Akatha vesi lomalizira, akalinde adzatsogoza opita ku ubatizo kumalo omizira kapena ku magalimoto owapereka kumeneko. Popeza ubatizo ndi kusonyeza kudzipatulira kwa munthuwe komanso ndi nkhani yaumwini ya munthuwe ndi Yehova, palibe makonzedwe amene amatchedwa kubatizidwa ndi mnzako kumene obatizidwa aŵiri kapena oposerapo amakupatirana kapena kugwirana manja pobatizidwa.
Utumiki Wodzifunira: Chithandizo chodzifunira chimafunika kuti msonkhano wachigawo uyende mwamyaaa. Ngakhale ngati mungagwire ntchito masiku ena chabe amsokhanowo, ntchito yanu idzayamikiridwa kwambiri. Ngati mungathandize, chonde pitani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhanopo. Ana osafika zaka zakubadwa 16 nawonso angathandize kuti msonkhano ukhale wachipambano, koma ayenera kugwira ntchito ndi kholo kapena munthu wina wachikulire.
Mabaji: Chonde valani mabaji okonzedwa bwinowo pamsonkhano ndi pamene mukupita kapena kuchokera kumalo a msonkhano. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimatitheketsa kupereka umboni wabwino pamene tikuyenda. Mabaji ayenera kugulidwa kumpingo wanu, popeza kuti sadzakhalako kumisonkhano.
Zokudziŵikitsani: Kuwonjezera pa baji la Msonkhano Wachigawo wa “Mawu Aulosi a Mulungu” aliyense akulimbikitsidwa kukhala ndi khadi lake la Chidziŵitso kwa Dokotala. A banja la Beteli ndi apainiya ayeneranso kukhala ndi makadi awo owadziŵikitsa.
Mawu Ochenjeza: Mosasamala kanthu za kumene mwaimika galimoto lanu, muyenera kuikiya nthaŵi zonse ndipo musasiye mkati kanthu kalikonse pooneka. Kiyirani zinthu zanu m’buti ngati kuli kotheka. Ndiponso, chenjerani ndi mbala ndi opisa m’thumba, amene amakopeka ndi kusonkhana kwa anthu ambiri. Zimenezi zimaphatikizapo kusasiya chinthu chilichonse chamtengo wapatali pampando popanda woyang’anira. Pakhala ngakhale malipoti angapo onena za zigaŵenga zimene zimayesa kunyengerera ana kufuna kuwaba pamsonkhano. Chonde samalani.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
Konzekerani kudzapezekapo tsiku lonse Lachisanu, Loŵeruka, ndi Lamlungu!