Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi zofalitsa ziti zimene tiyenera kuphunzira ndi achatsopano asanabatizidwe?
Munthu asanapatulire moyo wake kwa Yehova ndi kubatizidwa, ayenera kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka. (Yoh. 17:3) Adzapeza chidziŵitso chimene akufunikira mwa kuphunzira zonse ziŵiri bolosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Nthaŵi zambiri bolosha la Mulungu Amafunanji limaphunziridwa koyambirira. Komabe, ngati phunziro layamba ndi buku la Chidziŵitso, bolosha la Mulungu Amafunanji liyenera kuphunziridwa akamaliza kuphunzira buku. Chifukwa chiyani izi zili zofunika?
Bolosha la Mulungu Amafunanji limapereka chidule cha ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Ngati liphunziridwa koyambirira, lidzapangitsa wophunzira kudziŵa zinthu zoyambirira zofunika pokondweretsa Yehova. Ngati liphunziridwa komalizira, lidzakhala ngati chida chothandizira kubwereza zimene zinaphunziridwa m‘buku la Chidziŵitso. Ponse paŵiri, limbikitsani wophunzira kuŵerenga malemba amene aperekedwa ndi kuwalingalira. Onetsetsani kuti mwakambirana zithunzi, popeza ndi zida zabwino kwambiri zophunzitsira.—Onani Nsanja ya Olonda ya January 15, 1997, masamba 16-17.
Pamene wophunzira wamaliza kuphunzira zofalitsa ziŵirizi, akhoza kuyankha mafunso onse amene akulu adzakambirana naye pokonzekera ubatizo. Ngati zatero, sikukakhala koyenera kuchita nayenso phunziro m’buku lina lililonse, ngakhale kuti mphunzitsiyo adzapitiriza kukhala ndi chidwi ndi kupita kwake patsogolo.—Onani Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, masamba 14, 17.