Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/00 tsamba 3-4
  • April—Nthaŵi Yokhala Achangu pa Ntchito Zokoma!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April—Nthaŵi Yokhala Achangu pa Ntchito Zokoma!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Zofunika Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Zokumbutsa za Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 4/00 tsamba 3-4

April—Nthaŵi Yokhala Achangu pa Ntchito Zokoma!

1 Pamene mphepo yamkuntho ili pafupi kuwomba kumalo amene kumakhala anthu, kuchenjeza anthu zatsokalo kumakhala kofunika kwambiri. Mphepo yamkuntho ikayandikira, m’pamene kumafunikanso kuchenjeza mwamphamvu zedi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti miyoyo ili pangozi! Anthu ena angakhale kuti sanamve kuchenjeza kwa nthaŵi yam’mbuyomo. Ena angakhale atamva koma atanyozera kuchitapo kanthu. Zili chimodzimodzinso ndi chenjezo la Mulungu limene tatumidwa kuti tichenjeze, “kavumvulu” wa mkwiyo wolungama wa Mulungu asanasese mbali zonse za dziko loipali. (Miy. 10:25) Miyoyo yosatha ya mabiliyoni a anthu ili pachiswe! Tikufunika kuchenjeza. Tiyenera kukhala “achangu pa ntchito zokoma.”—Tito 2:11-14.

2 Kwa zaka zambiri, anthu a Yehova akhala akusonkhezeredwa kuona nyengo ya Chikumbutso kukhala nthaŵi yosonyeza changu chapadera muutumiki. M’ngululu ya 1939, Informant, umene tsopano ndi Utumiki Wathu wa Ufumu, unali ndi chilimbikitso ichi: “Popeza ngululu ndiponso nyengo yabwino yayamba, tiyenera kuyembekezera kuti ofalitsa mumpingo aŵirikiza maola a muutumiki wakumunda, ndiponso nthaŵi ya apainiya ichuluka kwambiri. Mwezi wa April uli ndi masabata asanu. Ulinso ndi masiku a Loŵeruka asanu. Pangani Loŵeruka ndi Lamlungu lililonse mu April . . . kukhala nthaŵi yapadera yochitira umboni.” Chimenecho ndicho chinali cholinga chabwino kwa abale athu zaka 60 zapitazo! Chaka chino, monga 1939, mwezi wa April uli ndi masabata asanu athunthu. Kodi mwakonza zotani mwezi uno? Mwalemba zotani pa kalendala yanu ya April 2000? Konzani zogwira ntchito yokoma pamodzi ndi anthu a Yehova ena onse mokwanira m’mwezi wapadera umenewu wochita ntchito yachangu yauzimu.

3 Zimene Tikuyembekezera Kukwaniritsa: Tsiku lofunika kwambiri m’chaka cha 2000 lili m’mwezi uno. Tsiku lokumbukira imfa ya Yesu ndilo pa April 19. Tiyeni tiyesetse mwakhama kuitanira anthu ambiri mmene tingathere ku Chikumbutso. Monga mmene tinanenera mwezi watha, lembani ndandanda ya onse amene mukuona kuti angabwere ku Chikumbutso ndipo onetsetsani kuti palibe amene mwam’phonya. Anthu oitanidwawo ayenera kuphatikizapo wofalitsa aliyense wofooka, ophunzira Baibulo, maulendo obwereza, amene kale anali kuphunzira, ogwira nawo ntchito, akusukulu anzathu, anansi, achibale, ndi anthu ena odziŵana nawo. Madzulo a tsiku la Chikumbutso, tonsefe tidzakhala ndi mwayi wocheza ndi amene abwera kuti aone kuti alandiridwa. Chikumbutso chikatha, tingapitekonso ndi thandizo lowonjezera lauzimu kwa anthu achidwi otereŵa.

4 Kukhala “achangu pa ntchito zokoma” masiku a Chikumbutso asanafike ndiponso Chikumbutso chitatha ndi njira yabwino kwambiri yom’sonyeza Yehova kuti timayamikira kwambiri zonse zimene watichitira. Ngati ndinu mpainiya wothandiza, mudzafuna kuyesetsa kuti muthere maola 50 kapena kuposerapo muutumiki. (Mat. 5:37) Tsatirani kwambiri ndandanda imene munapanga kumayambiriro a mwezi uno. (Mlal. 3:1; 1 Akor. 14:40) Tonsefe tichite zimene tingathe kuthandiza apainiya onse, mwa kuwalimbikitsa ndi kugwira nawo limodzi ntchito m’munda. (Yerekezani ndi 2 Maf. 10:15, 16.) Ngati tifesa mwachangu mu April, tingayembekezere kupeza chimwemwe chochuluka ndi madalitso a Yehova. (Mal. 3:10) Mwina izi zidzatsogolera kupitiriza upainiya wothandiza kapena kuyamba upainiya wokhazikika. Changu chauzimu chimene tichite mu April chipitirire ndithu m’miyezi yotsatira tikumapitiriza kukhala ofalitsa Ufumu okhazikika.

5 Mosakayikira, anthu a Yehova ambiri mwezi uno ayambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba ambiri. Kodi mukufuna mutayambitsa lanu? Pempherani makamaka za nkhani ya phunziro, ndipo gwirani ntchito mogwirizana ndi mapemphero anuwo. Tsimikizani kuti Yehova adzayankha mapemphero anu odzichepetsa ofuna kupeza anthu owongoka mitima oti muwaphunzitse.—1 Yoh. 3:22.

6 Naka kafikidwe ka m’munda kamene kakhala kogwira ntchito kwambiri kuyambitsira zokambirana. Yambani ndi kufunsa kuti: “Kodi muganiza kuti chipolowe chonse chimene chikuchitika m’masukulu chikuchitika chifukwa cha ziwanda kapena chifukwa cha kupereŵera kwa malangizo a makolo?” Yembekezani Yankho. Ngati munthu anena kuti “zochita za ziwanda,” ŵerengani Chivumbulutso 12:9, 12, ndipo gogomezerani zochita za Mdyerekezi pochirikiza chisokonezo m’dziko lapansi. Ndiyeno tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji paphunziro 4, m’funseni ngati anayamba walingalira kumene kunachokera Mdyerekezi. Pitirizani kuŵerenga ndipo kambiranani ndime ziŵiri zoyambirira m’nkhaniyi. Ngati munthuyo ayankha kuti “kupereŵera kwa malangizo amakolo” kukhala chifukwa chake m’masukulu muli zipolowe, ŵerengani 2 Timoteo 3:1-3 ndipo tchulani mikhalidwe imene mwachionekere imachirikiza vutoli. Ndiyeno tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji paphunziro 8, ŵerengani ndime 5, ndiyeno pitirizani kukambirana. Ngati mugwirizane kuti mudzabweranso, ndiye kuti mukulambula njira ya phunziro la Baibulo lokhazikika ndi munthuyo. Pa ulendo wobwereza, m’funseni ngati akudziŵa aliyense amene angasangalale kumva zimene akuphunzirazo.

7 Njira ina imene tingakhalire “achangu pa ntchito zokoma” mu April ndiyo kuchita nawo njira zosiyanasiyana za ulaliki. Kodi munayamba mwalingalirapo zokachitira umboni koimika mabasi kapena ku siteshoni ya sitima? Kapena mungakonde kuyesa kulalikira pamsewu, kapena m’gawo la anthu a malonda? Bwanji osachita zimenezi mwezi uno? Yehova adzakuthandizani kuti mukhale olimba mtima. (Mac. 4:31; 1 Ates. 2:2b) Mwinamwake mungagwirizane kudzayendera limodzi ndi mpainiya kapena wofalitsa amene ali wozoloŵera mbali zimenezi zautumiki.

8 Aliyense wofuna kuwonjezera mbali yake mu ntchito yolalikira angafunike kuchita nawo ulaliki wamwamwayi. Nthaŵi zambiri, chomwe chimafunika ndi kukambirana ndi munthuyo mwaubwenzi. Kungofunsa funso limene lili lochititsa chidwi basi, mwina kugwiritsa ntchito limene lafotokozedwa mu ndime 6. Yesetsani kugwiritsa ntchito bwino ngakhale nthaŵi yochepa zedi imene ngati sitisamala ingapite pachabe. Sititaya ndalama za matambala kokha chifukwa chakuti n’zosakwana makwacha. Bwanji osagwiritsanso ntchito bwino kaya mphindi 5, 10, kapena 15 mukuchitira umboni wamwamwayi?

9 Nthaŵi Yolingalira: Lingalirani mfundo zazikulu zam’mbuyo zimene zinagogomezeredwa mu seŵero la pa Msonkhano Wachigawo wachaka chatha wa “Mawu Aulosi a Mulungu.” Seŵero lamutu wakuti, Kuyamikira Choloŵa Chathu Chauzimu, linatichititsa kulingalira mwakuya za kusiyana kwa Yakobo ndi Esau. Esau anati iye anali wokonda zinthu zauzimu monga Yakobo, koma ntchito za Esau sizinasonyeze zimenezi. (Gen. 25:29-34) Ndi chenjezo lamphamvu kwa ife bwanji! Monga Yakobo, tiyeni tikhale okonzeka kulimbana, ngakhale kumenyera nkhondo madalitso a Yehova. (Gen. 32:24-29) Bwanji osagwiritsa ntchito mwezi wa April ndi miyezi yotsatirayi kusula changu chathu, mwa kusaona choloŵa chathu chauzimu chapaderachi mwachibwanabwana?

10 “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.” (Zef. 1:14) Uthenga wabwino wa Ufumu uyenera kulalikidwa. Miyoyo ya anthu ili pangozi! Mwezi uno ukhaletu wa madalitso kwa anthu a Yehova tonse pamene mogwirizana tikusonyeza kuti tili “achangu pa ntchito zokoma.”

[Bokosi patsamba 4]

Zoyenera Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso

Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lachitatu, pa April 19. Akulu ayenera kusamalira zinthu izi:

◼ Poika nthaŵi ya msonkhano, onetsetsani kuti zizindikiro zisayendetsedwe dzuŵa lisanaloŵe.

◼ Aliyense, kuphatikizapo wokamba nkhani, ayenera kuuzidwa nthaŵi yeniyeni ndi malo kumene kudzachitikire mwambo umenewu.

◼ Muyenera kupezeratu mkate ndi vinyo zoyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.

◼ Mbale, makapu, tebulo labwino ndi nsalu zabwino zoyala patebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthaŵi yabwino.

◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayenera kuyeretsedweratu nthaŵi yabwino.

◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi otumikira ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsera zinthu.

◼ Mupange makonzedwe okapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense wodwala amene sangathe kupezekapo.

◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kotero kuti pasadzakhale kupanikizana kwa anthu pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena