Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
Timadziŵa kuti Yehova Mulungu n’ngwoyenera chikondi chathu chonse ndi kulambira kwathu konse. Komabe, dziko limafuna kutinyengerera kuti tisakhale naye paunansi wabwino. (Yoh. 17:14) Kuti tikulitse chikondi chathu pa Yehova ndiponso kuti atilimbikitse kukana zinthu za dziko zimene zingawononge uzimu wathu, msonkhano wadera wachaka chautumiki cha 2001 udzakhala ndi mutu wakuti “Kondani Mulungu—Osati Zinthu za Dziko.”—1 Yoh. 2:15-17.
Kukonda kwambiri Yehova kumatisonkhezera kuchitira umboni za iye. Komabe, anthu a Mulungu ambiri utumiki wakumunda umawavuta. M’nkhani yamutu wakuti “Kukonda Mulungu Kumatisonkhezera mu Utumiki Wathu,” mudzaphunzira mmene anthu ambiri agonjetsera manyazi ndi zododometsa zina n’cholinga chofuna kuchita nawo utumiki umenewu mokwanira.
Kodi mikhalidwe yoipa yadziko imatikhudza motani? Mikhalidwe imene kalelo inkaoneka kuti n’njoipa tsopano amati ndi mmene moyo wakhalira. Nkhani yakuti “Okonda Yehova Amadana ndi Choipa” ndiponso nkhani yosiirana yamutu wakuti, “Zinthu za M’dziko—Kodi Timadziona Motani?” zidzakulitsa kutsimikiza mtima kwathu kukana zilakolako zoipa.
Chitsanzo cha Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi Msonkhano wa Utumiki komanso chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo zidzaphatikizidwa m’pulogalamuyi. Nkhani yapoyera yakuti, “Mmene Chikondi ndi Chikhulupiriro Zimagonjetsera Dziko,” idzatilimbikitsa kutsanzira Yesu pokana zisonkhezero za dziko. (Yoh. 16:33) Onetsetsani kuti mwaitanira ophunzira Baibulo anu kuti adzapezekepo. Aliyense amene akufuna kubatizidwa ayenera kuuza woyang’anira wotsogolera mofulumira kuti akonze zofunikira.
Msonkhano wadera umenewu, udzaika malingaliro athu makamaka pamene payenera kugona chikondi chathu kuti tisangalale ndi madalitso ochuluka a Yehova. Musaphonye mbali iliyonse ya msonkhanowu!