Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 1 tsamba 12-13
  • Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani za Ufumu wa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Zokhudza Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 1 tsamba 12-13
Dziko lapansi likuwombedwa ndi dzuwa

Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi Ufumuwu ukuchita chiyani panopa? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuupempherera kuti ubwere?

Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

Luka 1:31-33: “Udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha.”

Mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankalalikira inali Ufumu wa Mulungu.

Mateyu 9:35: “Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”

Yesu anapatsa ophunzira ake chizindikiro chimene chingawathandize kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera.

Mateyu 24:7: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”

Panopa otsatira a Yesu akulalikira za Ufumu padziko lonse.

Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”

Mfundo Zokhudza Ufumu wa Mulungu

Kumene uli. Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene linakhazikitsidwa kumwamba ndi Mulungu.​—DANIELI 2:44; MATEYU 4:17.

Cholinga chake. Ufumu wa Mulungu udzasintha dzikoli n’kukhala Paradaiso ndipo anthu onse azidzakhala mwamtendere komanso mogwirizana. Anthu sazidzadwala kapenanso kufa.​—SALIMO 37:11, 29.

Olamulira ake. Mulungu anasankha Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wa kumwamba komanso anthu ena oti adzalamulire naye okwana 144, 000 ochokera padziko lapansi.​—LUKA 1:30-33; 12:32; CHIVUMBULUTSO 14:1, 3.

Nzika zake. Anthu omwe adzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu azidzakhala padziko lapansi, azidzagonjera ulamuliro wa Yesu komanso azidzamvera malamulo a Ufumuwo.​—MATEYU 7:21.

N’chifukwa Chiyani Yesu Ndi Mfumu Yoyenera Kulamulira Anthu?

Yesu ali padziko lapansi, anasonyeza kuti adzakhala wolamulira wabwino komanso wachikondi chifukwa

  • Ankasonyeza kuti amaganizira anthu osauka.​—LUKA 14:13, 14.

  • Ankadana ndi chinyengo komanso zinthu zopanda chilungamo.—MATEYU 21:12, 13.

  • Ankatha kulamulira mphamvu zam’chilengedwe.​—MALIKO 4:39.

  • Anadyetsa anthu masauzande ambiri.​—MATEYU 14:19-21.

  • Ankamvera chisoni odwala ndipo ankawachiritsa.​—MATEYU 8:16.

  • Ankaukitsa akufa.​—YOHANE 11:43, 44.

Mmene Ufumu wa Mulungu Ungakuthandizireni Panopa

Ngati mutakhala nzika ya Ufumu wa Mulungu mukhoza kukhala ndi moyo wosangalala ngakhale panopa. Mwachitsanzo, anthu amene ndi nzika za Ufumu wa Mulungu

  • ‘Amayesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu onse.’​—AHEBERI 12:14.

  • Okwatirana amakhala mwamtendere komanso mogwirizana chifukwa amakondana komanso kulemekezana.​—AEFESO 5:22, 23, 33.

  • Amakhala osangalala komanso okhutira chifukwa choti “amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—MATEYU 5:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena