Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/01 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Phunziro la Buku la Mpingo Limatithandizira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Phunziro Labuku Lampingo Limachirikiza Zochita Zophunzitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Chifukwa Chake Phunziro la Buku la Mpingo N’lofunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 4/01 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi nthaŵi yabwino kukhazikitsa malo ena a Phunziro la Buku la Mpingo ndi iti?

Muyenera kuganiza zokhazikitsa gulu latsopano nthaŵi imene mukuona kuti n’kofunika, kuti malo onse a phunziro la buku ndiponso ku Nyumba ya Ufumu azikhalabe ndi anthu 15 kapena kucheperapo. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera?

Magulu a Phunziro la Buku la Mpingo akakhala ochepa, wochititsa amatha kusamalira bwino aliyense wa m’gululo. Ndiponso, onse amakhala ndi mpata woyankha wokwanira pakuti malowo amakhala abwino kulengeza poyera chikhulupiriro chawo. (Aheb. 10:23; 13:15) Kukhala ndi magulu ang’onoang’ono m’gawo lonse la mpingo kumathandiza kuti kufika pa Phunziro la Bulu la Mpingo ndi misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda kukhale kosavuta. Mipingo imene ili ndi malo ambiri a phunziro la buku apeza kuti chiŵerengero chonse cha anthu opezeka paphunziro la buku chimakhalanso chochuluka.

Pangakhale zifukwa zapadera zimene zingapangitse kuti akhazikitse gulu lina, ngakhale kuti lidzakhala la anthu ochepa kwambiri. Izi zingachitike kumalo akutali kapena ngati magulu amene alipowo kuli anthu ambiri kapena malo ndi ochepa. Ngati n’kofunika angakhazikitse gulu losonkhana masana kuthandiza anthu okalamba, ogwira ntchito usiku kapena alongo amene amuna awo si Mboni.

Gulu lililonse la phunziro la buku liyenera kukhala ndi ofalitsa olimba ndi achangu mwauzimu angapo komanso wochititsa ndi woŵerenga woyeneretsedwa. Abale ayenera kuyesetsa kukwaniritsa zofunika zimenezi mu mpingo.

Akulu angathandize mpingo kupita patsogolo mwa kuona kuti magulu a phunziro la buku la mpingo ndi aang’ono bwino, osamalidwa bwino mwauzimu ndiponso kuti amachitikira pamalo abwino. Nthaŵi iliyonse imene mukuona kuti n’kofunika, mutha kukhazikitsa magulu atsopano kuti anthu onse apindule mokwanira ndi makonzedwe apadera ndi achikondi ameneŵa. Kodi mungapereke nyumba yanu kukhala malo a phunziro la buku? Anthu ambiri amene achita zimenezi adalitsidwa kwambiri mwauzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena