M’fikeni Pamtima Wophunzira Wanu
1 Yesu asanapite kumwamba anauza ophunzira ake kuti aphunzitse ena kuti “asunge” zinthu zonse zimene anawalamulira. (Mat. 28:19, 20) Kuti munthu “asunge” malamulo a Kristu, m’pofunika kuti zimene akuphunzirazo zim’gwire mtima. (Sal. 119:112) Kodi mungakhudze motani mtima wa amene mukuphunzira naye Baibulo?
2 Pemphani Yehova Kukutsogolerani: Ntchito yopanga ophunzira ndi ya Mulungu. Timabala zipatso osati chifukwa cha maluso athu koma chifukwa cha thandizo lake. (Mac. 16:14; 1 Akor. 3:7) Chotero, pophunzitsa ena choonadi m’pofunika kupempha Yehova kutithandiza.—Yes. 50:4.
3 Dziŵani Zikhulupiriro za Wophunzirayo: Kudziŵa zikhulupiriro za anthu ndiponso chifukwa chake amakhulupirira zimenezo kungatithandize kudziŵa zoti tinene kuti tiwafike pamtima. N’chifukwa chiyani wophunzirayo akukhulupirira chiphunzitso chinachake? Kodi cham’khutiritsa n’chiyani kuti zimenezo ndi zoona? Kudziŵa zimenezi kudzatithandiza kulankhula mozindikira.—Mac. 17:22, 23.
4 Kambiranani Nkhani Zanzeru za m’Malemba: Wophunzira azimvetsetsa kuti zimene akuphunzira n’zoonadi. (Mac. 17:24-31) Tinene zifukwa zomveka za chiyembekezo chathu. (1 Pet. 3:15) Koma nthaŵi zonse tichite zimenezi mokoma mtima ndiponso moleza.
5 Gogomezerani mwa Mafanizo: Sikuti mafanizo amangochititsa kuti wophunzira amvetse mosavuta koma amam’sonkhezeranso malingaliro. Mafanizo amakhudza maganizo ndi mtima womwe. Yesu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafanizo. (Marko 4:33, 34) Komabe, kuti fanizo likhale logwira mtima, liyenera kugwirizana ndi zimene tikukambiranazo komanso ndi moyo wa wophunzirayo.
6 Muuzeni Mapindu Olabadira Choonadi: Anthu amafuna kudziŵa mapindu ogwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Thandizani wophunzira wanu kuzindikira mfundo ya mawu a Paulo a pa 2 Timoteo 3:14-17.
7 Ngati ena sakulabadira zimene mukuphunzitsa, musagwe ulesi. Si mitima yonse imene ingalabadire. (Mat. 13:15) Komabe, ena adzakhulupirira. (Mac. 17:32-34) Khama lanu lofuna kuwafika anthu pamtima ndi uthenga wabwino, lithandizetu anthu ambiri kulabadira ndi ‘kusunga’ zimene Yesu analamula.