Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/01 tsamba 1
  • Musachite Mantha!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musachite Mantha!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Tingatani ndi Mavuto Amene Timakumana Nawo Muutumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Yehova Amakuganizirani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Kunyumba Ndi Nyumba”
    Imbirani Yehova
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 7/01 tsamba 1

Musachite Mantha!

1 Tikakonzeka kupita ku ulaliki wa kukhomo ndi khomo, vuto lalikulu si komwe tidzapita ayi, koma ifeyo. Tingachite mantha kunyamuka kukalankhula choonadi kwa “anthu onse” chifukwa chodziona kuti sitikuyenera. (1  Tim. 2:4) Koma sitiyenera kuopa kulalikira uthenga wabwino. Chifukwa chiyani sitiyenera kuopa?

2 Ndi Uthenga wa Yehova: Yehova wanena mawu ake m’Baibulo. Kuwauza ena uthenga umenewu, ndiko kuwauza malingaliro ake, osati athu. (Aroma 10:13-15) Anthu akakana uthenga wa Ufumu, ndiye kuti akukana Yehova. Komabe, sitigwa ulesi. Tikukhulupirira kuti uthenga umenewu udzakhudza mitima ya anthu ofunitsitsa kuti mikhalidwe isinthe padziko lapansi ndiponso ya anthu ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.—Ezek. 9:4; Mat. 5:3, 6.

3 Yehova Amakoka Anthu: Munthu amene nthaŵi ina anakana kumvetsera zonena zathu, tsopano angamvetsere chifukwa mikhalidwe yake yasintha ndipo mtima wake wafeŵa. Tsopano Yehova angam’komere mtima munthu wotereyu ndi ‘kum’koka.’ (Yoh. 6:44, 65) Zikatere, tizikonzekera kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova ndiponso kutsogozedwa ndi angelo kwa anthu otereŵa.—Chiv. 14:6.

4 Mulungu Amatipatsa Mzimu Wake: Mzimu woyera umatithandiza kunena ‘molimba mtima mwa Ambuye.’ (Mac. 14:1-3) Popeza kuti mu utumiki wathu timakhala ndi otithandiza amphamvu ameneŵa, tisachite mantha kuuza choonadi anansi athu, ogwira nawo ntchito, anzathu akusukulu, achibale kapena anthu ophunzira kwambiri ndi olemera.

5 Yesu Anatiphunzitsa Momwe Tingachitire: Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso opangitsa munthu kuganiza, mafanizo osapita m’mbali ndiponso mfundo za m’Malemba. Ankafotokoza choonadi mosavuta, mosangalatsa ndiponso mochokera pansi pa mtima. Zimenezi zidakali njira zabwino kwambiri lerolino. (1 Akor. 4:17) Tingalalikire m’mikhalidwe yosiyanasiyana, koma uthenga wamphamvu wa Ufumu susintha.

6 Tili ndi mwayi kuti Yehova akutigwiritsira ntchito yothandiza anthu m’njira yapadera ndiponso yofunika kwambiri. Tisachite mantha! Tikhaletu olimba mtima ndipo Yehova “atitsegulire ife pakhomo pa mawu” kuti tiuze ena uthenga wabwino.—Akol. 4:2-4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena