Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/01 tsamba 8
  • Kodi Mungatumikire ku Gawo Losoŵa Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatumikire ku Gawo Losoŵa Kwambiri?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Abrahamu Anali Chitsanzo cha Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Tate wa Onse Okhala ndi Chikhulupiriro”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Chikhulupiriro Chinamufulumiza ku Ntchito
    Galamukani!—1988
  • Khalani ndi Chikhulupiriro Monga cha Abrahamu!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 7/01 tsamba 8

Kodi Mungatumikire ku Gawo Losoŵa Kwambiri?

1 Kodi munayamba mwalingalirapo zosamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri? Kodi mutapemphedwa ‘kuoloka . . . kukathangata,’ mungachite monga anachitira mtumwi Paulo? (Mac. 16:9, 10) M’mipingo yambiri mukufunika mabanja okhwima mwauzimu kapena apainiya kuti athandize kufola gawo ndiponso akulu ndi atumiki otumikira oyeneretsedwa kuti akathandize kutsogolera. Gawo lake lingakhale dera lalikulu la midzi ing’onoing’ono ya patalipatali. Nyumba ya Ufumu yapafupi ingapezeke kutali kwambiri. Ntchito yolembedwa ingakhale yosoŵa. Nthaŵi zina nyengo ingakhale yoipa. Kodi mungalole m’mikhalidwe ngati imeneyi? Kodi mungapirire bwanji zoterezi?

2 Chikhulupiriro Ndiponso Chidaliro N’zofunika: Abramu atauzidwa ndi Mulungu anachoka m’tauni yakwawo ya Uri ndi mkazi wake, mphwake ndiponso Tera, bambo ake okalamba. Ndipo anayenda mtunda wamakilomita 1,000 kupita ku Harana. (Gen. 11:31, 32; Neh. 9:7) Tera atamwalira, Yehova anauza Abramu amene tsopano anali ndi zaka 75, kuchoka ku Harana, kusiya abale ake kuti apite kudziko limene akam’sonyeza. Abramu, Sarai ndiponso Loti ‘anatuluka.’ (Gen. 12:1, 4, 5) Ndi zoona kuti Abramu sanasamuke n’cholinga chokatumikira ku gawo limene linali losoŵa kwambiri atumiki. Koma kuti asamuke panafunika chinachake. Kodi panafunika chiyani?

3 Kuti Abramu achite zimenezi anafunika chikhulupiriro ndiponso chidaliro. Anafunika kusintha maganizo ndiponso moyo wake. Anafunika kusiya abale ake amene anali kumuteteza. Komabe anakhulupirira kuti Yehova adzam’samala pamodzi ndi banja lake. Lerolino anthu ambiri asonyeza kukhulupirira kwawo Yehova mwanjira yofananayi.

4 Ntchito ya Nthaŵi Yochepa: Kodi munalawako madalitso amene amadza mwa kulalikira m’magawo osagaŵiridwa? Ku United States of America, mbale wina wa ku California amene anapita ku Utah analemba kuti: “Atandipempha kuti ndipite ndi anthu ena ku gawo lofoledwa mwa kamodzikamodzi, ndinazengereza. Koma ndinaganiza zovomera ntchitoyo. Sindinong’oneza bondo kuti ndinachita zimenezi komanso zimenezi zinasintha moyo wanga. Tsiku lililonse ndimathokoza Yehova kuti ndinali nawo paulendo umenewu.” Mbale wa ku Florida amene anapita ku Tennessee anati, nthaŵi imene anapita ku gawo lofoledwa mwa kamodzikamodzi ndi yosaiŵalika pa zaka 20 zimene wakhala m’choonadi. Mnyamata wa ku Connecticut amene anapita ku West Virginia anati: “Kulalikira ku gawo losoŵa chinali chinthu chabwino kwambiri m’moyo wanga!” Ofalitsa ambiri akuvomereza kuti kutumikira ku gawo losoŵa kwambiri ngakhale kwa nthaŵi yochepa kwawonjezera kuyamikira kwawo utumiki. Lankhulani ndi amene anachitapo zimenezi. Mudzaona kuti analimbikitsidwa mwauzimu ndipo mosakayikira adzachitanso zimenezi ngati atapatsidwa mwayi wina.

5 Kuvomera kukagwira ntchito kwanthaŵi yochepa ku gawo losoŵa kwambiri kumathandizanso m’njira ina. Anthu amene amachita zimenezi amapeza malangizo abwino owathandiza ‘kuŵerengera mtengo’ wosamukira kudera lina la dziko.—Luka 14:28.

6 Yehova akufuna kuti uthenga wabwino ulengezedwe “padziko lonse lapansi” chimaliziro chisanafike. (Mat. 24:14) Popeza mwadziŵa zimenezi, kodi mudzakhala wofunitsitsa kusamukira ku gawo losoŵa kwambiri ngati mungathe? Magawo osoŵa alaliki okwanira alipo ambiri.

7 Kusamukira ku Gawo Losoŵa Kwambiri: Kodi munapuma pantchito? Kodi muli ndi njira yodalirika yopezera ndalama? Ngati si choncho, kodi mungachite bizinesi? Ngati simungasamuke, kodi mungathandize wina m’banjamo kukatumikira kwina?

8 Ngati mwalingalira mwapemphero ndipo mukuona kuti mungasamukire ku gawo losoŵa kwambiri, kambiranani nkhaniyi ndi banja lanu komanso akulu a mu mpingo wanu. Ndiyeno, lembani kalata ndipo apatseni akulu kalatayo kuti alembeponso malingaliro awo ndi zofunika zina, asanaitumize ku ofesi ya nthambi.

9 Kodi n’ziti zofunikanso kulemba m’kalatamo? Zaka zanu, tsiku limene munabatizidwa, maudindo anu mu mpingo, kaya ndinu wokwatira kapena mbeta ndiponso ngati muli ndi ana aang’ono. Tchulani komwe mukufuna kukatumikira, malinga ndi zosoŵa zanu.

10 Kodi ndinu wachidwi ndiponso wokonzeka? Kodi mikhalidwe yanu ikukulolani kukatumikira ku gawo losoŵa kwambiri? Ngati n’choncho, mudzaona mmene Yehova nthaŵi zonse amadalitsira kwambiri anthu amene amam’khulupirira, pamene akusonyeza mzimu wodzimana.—Sal. 34:8; Mal. 3:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena