Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct. 15
“Kodi pakufunika chiyani kuti dzikoli likhale labwino ndi lachimwemwe? [Yembekezerani yankho.] Anthu ayesa maboma osiyanasiyana kuti zinthu zisinthe. Koma onani maganizo a Mulungu pankhaniyi. [Ŵerengani Yeremiya 10:23.] Nkhani iyi ikutchula ‘Chimene Chidzabweretse Dziko Lachimwemwe,’ ndiponso momwe zimenezi zidzachitikire posachedwapa.”
Galamukani! Nov. 8
“Mungandivomereze kuti masiku ano anthu ali pamavuto kusiyana ndi kale, kodi si choncho? [Yembekezerani yankho.] Baibulo linaneneratu zimenezi. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1.] Anthu ambiri amapeza mavuto ochuluka m’moyo moti amadzipha. Magazini iyi ili ndi thandizo lenileni. Ikusonyeza momwe tingathetsere nkhaŵa ndi mmene tingasangalalire ndi moyo.”
Nsanja ya Olonda Nov. 1
Mukatha kutchula nkhani yomvetsa chisoni, funsani kuti: “N’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zoipa ngati zimenezi? Tonse tikudziŵa zabwino ndi zoipa, koma anthu akuchitabe zinthu zoipa. Chifukwa chiyani? [Akayankha, ŵerengani Chivumbulutso 12:9.] Magazini iyi ikufotokoza mmene tingadzitetezere mwa kuteteza chikumbumtima chathu.”
Galamukani! Nov. 8
“Mosakayikira mukuvomereza kuti tikukhala mu nthaŵi za mavuto. [Akayankha, ŵerengani 2 Timoteo 3:3.] Nthaŵi zambiri ‘ukali’ umachitika ndi m’banja momwe. Nkhani iyi yakuti, ‘Kuthandiza Akazi Amene Amamenyedwa ndi Amuna Awo,’ ili ndi uthenga wolimbikitsa. Mwina pali amene mungamuuze uthenga wolimbikitsa umenewu.”