Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2002
1 Anthu ambiri amaliona mopepuka luso la kulankhula. Koma ndi Yehova amene anatipatsa mphatso ya kulankhula. Imatithandiza kuti tilankhule ndi anthu ena ndiponso kunena maganizo athu ndi mmene tikumvera. Chachikulu koposa zonsezi n’chakuti tingatamande nako Mulungu wathu.—Sal. 22:22; 1 Akor. 1:4-7.
2 Amuna, akazi, ndi ana amaphunzira kulalikira dzina la Yehova mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase. (Sal. 148:12, 13) Pulogalamu ya sukulu ya 2002 ili ndi nkhani za m’Baibulo zambiri zimene aliyense angapindule nazo ndi kuzigwiritsa ntchito mu utumiki. Mwa kukonzekera ndi kutenga nawo mbali m’sukuluyi, zimene timadziŵa ndiponso luso lathu monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu zidzawonjezeka.—Sal. 45:1.
3 Ŵerengani Baibulo Tsiku ndi Tsiku: Ngati tili ndi Baibulo pafupi, nthaŵi iliyonse imene tapeza mpata tingaigwiritse ntchito poliŵerenga. Ambirife tsiku lililonse timakhala ndi mphindi zingapo zimene timapeza mpata woti titha kuugwiritsa ntchito kuŵerenga Baibulo. N’kopindulitsa kwambiri kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse tsamba limodzi. Kuŵerenga tsamba limodzi patsiku n’kokwanira kuti tiyendere limodzi ndi pulogalamu yoŵerenga Baibulo ya pandandanda ya Sukulu.—Sal. 1:1-3.
4 Luso loŵerenga bwino Baibulo lingatithandize kuwafika pamtima anthu amene timalankhula nawo ndi kuwalimbikitsa kutamanda Yehova. Abale amene amakamba nkhani Na. 2 mu sukulu ayenera kuyeserera, kuyeserera, kuyeserera kuŵerenga nkhaniyo mokweza. Woyang’anira sukulu adzayamikira ndi kunena malingaliro a momwe wophunzirayo angawongolerere kuŵerenga kwake.
5 Gwiritsani Ntchito Buku la Kukambitsirana: Nkhani Na. 3 ndi Na. 4 zidzachokera mu buku la Kukambitsirana. Ambirife tingafunike kuyesetsa kuti tizigwiritsa ntchito kwambiri chida chothandizachi mu utumiki wakumunda. Alongo ayenera kusankha njira zokambirana zimene zili zogwirizana ndi gawolo. Woyang’anira sukulu azionetsetsa momwe amaphunzitsira ndi kugwiritsira ntchito Malemba.
6 Sukulu ya Utumiki Wateokalase itithandizetu tonse kupitiriza kugwiritsa ntchito mphatso yopatsidwa ndi Mulungu imeneyi polalikira uthenga wabwino ndiponso potamanda Yehova, Mulungu wathu wamkulu.—Sal. 34:1; Aef. 6:19.