Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/02 tsamba 5
  • “Mphatso mwa Amuna” Zimaŵeta Gulu la Mulungu Mokondwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mphatso mwa Amuna” Zimaŵeta Gulu la Mulungu Mokondwa
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Thandizani Osochera Kubwerera M’gulu la Nkhosa
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Muzimvera Abusa Amene Yehova Watipatsa
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 3/02 tsamba 5

“Mphatso mwa Amuna” Zimaŵeta Gulu la Mulungu Mokondwa

1 Ndi dongosolo labwino kwambiri kuti Yehova mwa Mwana wake anatipatsa “mphatso mwa amuna.” (Aef. 4:8, 11, 12, NW) Zili ndi ntchito zambiri, komanso kuŵeta gulu la Mulungu mwachangu ndi mokondwa. (1 Pet. 5:2, 3) Tonse timapindula nalo dongosolo lofunika kwambiri limeneli. Kaya ena ali m’mavuto, ndi atsopano mu mpingo, ali ndi zoofoka zina, kapena asochera, amuna ameneŵa amafunira anthu onse moyo wabwino wauzimu.—Afil. 2:4; 1 Ates. 5:12-14.

2 Tikakhala ndi mantha chifukwa cha zinthu zosautsa zochitika m’dziko, abusa aang’ono ameneŵa amakhala “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.” Tikatopa kapena tikalemedwa ndipo tikufunika chilimbikitso, amatipatsa mpumulo, “monga mitsinje yamadzi m’malo ouma” kapena “monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Yes. 32:2.

3 Kulimbikitsa Osagwira Ntchito: Akulu amayesetsa kulimbikitsa ofalitsa osakhazikika kapena osagwira ntchito, kuwathandiza kuti ayambirenso kuchita nawo ntchito yonse ya mpingo mokhazikika. Maulendo aubusa osonyeza kukoma mtima kwawo athandiza anthu ambiri kumapezeka pamisonkhano ya mpingo nthaŵi zonse ndi kulimba mwauzimu kufika poti ayambanso kuloŵa nawo mu utumiki wakumunda. Ntchito yonseyi imene akulu amachita ndi umboni wakuti Yehova amatisamala ndipo amatikonda. Imasonyezanso kuti Yesu Kristu akutsogolera. Iye anapereka chitsanzo cha mmene abusa angasonyezere chikondi chimenechi kwa nkhosa yake iliyonse yosochera kapena yotayika.—Mat. 18:12-14; Yoh. 10:16, 27-29.

4 Abusa aang’ono amayang’ana zizindikiro za munthu amene akufooka mwauzimu. Aliyense amene akuoneka kuti wagwa mphwayi, wayamba kusonkhana mosakhazikika, kapena amene akufooka mu utumiki wakumunda amakhala kuti akufunika kuwathandiza mwauzimu. Akulu amakonda kuthandiza aliyense amene wayamba kutengera kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwa anthu akudziko kapena amene amakonda kunena zosuliza mpingo. Akulu achikondi ‘amapereka moyo wawo’ mwaufulu kuti athandize anthu otero kuyambiranso kukonda Yehova. Amachita zimenezi chifukwa chakuti amawafunira zabwino ndiponso chifukwa chakuti amawakonda kwambiri.—1 Ates. 2:8.

5 M’mbuyomu, Akristu ena odzipatulira anasiya kusonkhana ndi mpingo, anafooka mwauzimu chifukwa cha matenda, vuto la zachuma, kapena mavuto a m’banja. Akulu ameneŵa sanyoza anthu otereŵa koma amawatsimikizira mokoma mtima kuti Yehova amasamala nkhosa zake zonse ndipo amazithandiza pamavuto. (Sal. 55:22; 1 Pet. 5:7) Abusa atcheru a gulu la nkhosa angawathandize kuzindikira kuti ‘akayandikira kwa Mulungu, iye adzayandikira kwa iwo,’ ndipo adzawalimbikitsa ndi kuwapatsa mpumulo.—Yak. 4:8; Sal. 23:3, 4.

6 Kuyamikira Okalamba: Abusa aang’ono achikondi amakondanso anthu amene amanyalanyazidwa. Mu mpingo uliwonse muli anthu ena okalamba kapena opunduka. Zimene anthu ameneŵa amachita mu ntchito yolengeza uthenga wa Ufumu n’zochepa chifukwa cha mavuto awo. Mwina amalalikira kukabwera odzawaona kapena owasamalira basi. Komabe, zilizonse zimene angathe kuchita zimathandiza kwambiri ntchito yolalikira.—Mat. 25:15.

7 “Mphatso mwa amuna” zimadziŵa bwino kwambiri zosoŵa zauzimu za abale awo panyengo ino ya Chikumbutso. Ndi nthaŵi yabwino kwa akulu kuyesetsa kuthandiza onse amene asochera kupezanso chimwemwe ndi kuti mtima wawo upeze mtendere, zimene zimachitika chifukwa cha mayanjano olimbikitsa mumpingo. Timasangalala kwambiri tikaona “a pa banja la chikhulupiriro” ameneŵa akufika pa misonkhano ya mpingo ndiponso kupita mu utumiki wakumunda kukalengezanso chikhulupiriro chawo mu nsembe ya dipo.—Agal. 6:10; Luka 15:4-7; Yoh. 10:11, 14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena