Chikhulupiriro Chathu Chimatilimbikitsa Kuchita Ntchito Zabwino
1 Chikhulupiriro chinachititsa Nowa, Mose, ndi Rahabi kuchita kanthu kenakake. Nowa anamanga chingalawa. Mose anakana kusangalala kwanthaŵi yochepa m’nyumba ya Farao. Rahabi anabisa azondi ndipo kenako anamvera malangizo awo, zimene zinapulumutsa banja lake. (Aheb. 11:7, 24-26, 31) Kodi chikhulupiriro chathu lerolino chikutilimbikitsa kuchita ntchito zabwino zotani?
2 Kulalikira: Chikhulupiriro chimatilimbikitsa kulankhula za Mulungu wathu wabwino ndiponso zimene wakonza kuti tidzasangalale kosatha. (2 Akor. 4:13) Nthaŵi zina, tingamachite mphwayi ndi kulalikira. Koma ‘tikaika Yehova patsogolo pathu nthaŵi zonse,’ timalimbikitsidwa ndipo mantha amatha. (Sal. 16:8) Ndiyeno chikhulupiriro chathu chimatilimbikitsa kuwauza uthenga wabwino achibale, achinansi, anzathu akuntchito, anzathu a kusukulu, ndiponso anthu ena, panthaŵi iliyonse yabwino.—Aroma 1:14-16.
3 Kusonkhana Pamodzi: Kupezeka pa misonkhano mokhazikika ndi inanso mwa ntchito zabwino za chikhulupiriro. Chifukwa? Chifukwa chakuti kumasonyeza kuti timakhulupirira kuti Yesu amasonkhana nawo pamisonkhano yachikristu, mwa mzimu woyera wa Mulungu. (Mat. 18:20) Kumasonyeza kuti timafunitsitsa ‘kumva chimene Mzimu ukunena kwa Mipingo.’ (Chiv. 3:6) Timagwiritsa ntchito malangizo amene timalandira popeza timakhulupirira kuti akutiphunzitsa ndi Yehova, Mlangizi wathu Wamkulu.—Yes. 30:20.
4 Zosankha Zathu: Kukhulupirira kwambiri zinthu zimene sitiziona, kumatilimbikitsa kutsogoza zinthu zauzimu pamoyo wathu. (Aheb. 11:1) Izi nthaŵi zambiri zimatanthauza kusiya chuma. Mwachitsanzo, mbale winawake amene ndi mkulu mu mpingo anakana kukwezedwa pantchito chifukwa akanatero bwenzi akulephera kupezeka pa misonkhano ina ya mpingo. Ndiponso bwenzi akuchoka kukagwira ntchito kutali ndi kumene kuli banja lake, komanso akanasiya utumiki wa upainiya. Tiyeni ifenso tikhulupirire kwambiri zimene Baibulo limatiuza kuti Yehova adzapatsa anthu amene ‘amathanga afuna Ufumu wake ndi chilungamo chake,’ zofunika pamoyo wawo.—Mat. 6:33.
5 Anthu amaona momwe chikhulupiriro chimakhudzira moyo wathu. Inde, chikhulupiriro chathu n’chodziŵika padziko lonse lapansi. (Aroma 1:8) Chotero, tiyeni tonsefe tisonyeze mwa ntchito zabwino kuti chikhulupiriro chathu n’chamoyo.—Yak. 2:26.