‘Nthaŵi Zonse Tsatirani Chokoma’
1 ‘Nthaŵi zonse kutsatira chokoma kwa anthu onse’ ndiwo moyo wachikristu. (1 Ates. 5:15) Popita ku misonkhano yathu yachigawo, timakhala ndi mipata yambiri yochitira anthu ena zokoma. Nthaŵi zimenezi anthu amayang’ana ife, ndipo onse amene timakumana nawo amationa kukhala anthu abwino kapena oipa malinga ndi zimene tawachitira. Kuti mbiri yathu ikhalebe yabwino monga Mboni za Yehova, zochita zathu zisonyeze kuti ‘timachitira ulemu anthu onse.’ (1 Pet. 2:17) Kuchita zimenezi kumaphatikizapo ‘kusapenyerera zathu zokha, koma kupenyereranso za anzathu.’—Afil. 2:4.
2 Chaka chilichonse timalandira malangizo abwino otikumbutsa khalidwe loyenera tikakhala pamsonkhano. Chifukwa chiyani amachita zimenezi? Chifukwa chakuti khalidwe, kavalidwe, ndiponso zochita za dzikoli zikuipiraipirabe, sitifuna kutengera zochita zake. Sitikufuna kuti mbiri yathu yabwino iwonongeke. (Aef. 2:2; 4:17) Tiyeni tizikumbukira malangizo aŵa.
3 Phunzitsani Ana Kuchita Zokoma: Nthaŵi zina, ana amene amasiyidwa okha pamsonkhano popanda munthu wamkulu wowayang’anira, amayambitsa mavuto. (Miy. 29:15) Nthaŵi zina, makolo amagwira ntchito zina n’kusiya ana awo pamsonkhano popanda wowayang’anira. Ana ena amayamba kupulupudza kwambiri moti akalinde amaona kuti ndi bwino kuwaletsa kugwiritsa ntchito zinthu zina. Zimenezi zingasokoneze anthu ena.
4 Makolo, msonkhano usanafike, ndi bwino kukhala ndi nthaŵi yophunzitsanso ana anu khalidwe lachikristu limene afunika kusonyeza nthaŵi zonse ndiponso kulikonse kumene ali. (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, auzeni kuti chikondi chenicheni chachikristu, “sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” (1 Akor. 13:5) Anthu achikulire angagogomezere mawu ameneŵa mwa kuonetsa chitsanzo chabwino. Ananu, mungatsatire chokoma mwa kumvera makolo anu, kulemekeza zimene akonza pamsonkhanowo, ndi kuganizira anthu amene mwayandikana nawo. (Akol. 3:20) Tikayesetsa tonse kuchitira onse chokoma, ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.
5 Khalidwe lathu labwino limathandiza kwambiri anthu otiona komanso amene amatinyoza pazifukwa zosiyanasiyana. Zochita zathu zonse pamsonkhano ndi mu mzinda wa msonkhanowo, kaya tikuyenda mu msewu, kudya m’lesitilanti, kaya tikufuna kugwiritsa ntchito mpata umene wapezeka kuchitira umboni wa mwamwayi—zolankhula ndi zochita zathu monga Akristu zisonyeze kuti tikufuna kutsatira chokoma.
[Bokosi patsamba 4]
Kumbukirani:
■ Kuleza mtima ndi kulemekeza akalinde.
■ Kuyang’anira kwambiri zimene ana anu akuchita.