Olumala Komabe Obala Zipatso
1 Ngati ndinu mmodzi mwa anthu ambiri a Mboni za Yehova amene ndi olumala, mungachitebe utumiki wobala zipatso. Ndipotu, vuto lanulo lingakupatseni mpata wapadera wolalikira ndi kulimbikitsa ena.
2 Kulalikira: Anthu ambiri amene ndi olumala akuchita zambiri mu utumiki. Mwachitsanzo, mlongo wina amene amavutika kwambiri kuyenda ndi kulankhula chifukwa cha opaleshoni imene anachitidwa, anaona kuti angachite nawo ntchito yogaŵira magazini, mwamuna wake ataimika galimoto yawo m’mphepete mwa msewu wa anthu ambiri oyenda pansi. Nthaŵi ina, anagaŵira magazini 80 m’maola aŵiri okha. Vuto lanulo lingakupangitseni kukumananso ndi anthu amene amavuta kuwapeza m’njira zina. Ngati ndi choncho, atengeni kukhala gawo lanu lapadera.
3 Kulalikira kwanu kungakhale kogwira mtima kwambiri. Ena akamaona kulimbikira kwanu ndiponso mmene mfundo za m’Baibulo zakuthandizirani pamoyo wanu, angakopeke ndi uthenga wa Ufumu. Ndiponso, mukakumana ndi anthu amene akuvutika, zimene inu mwaona pamoyo wanu zingakuthandizeni kuwalimbikitsa ndi Mawu a Mulungu.—2 Akor. 1:4.
4 Limbikitsani Ena: Kodi nkhani ya moyo wa Laurel Nisbet amene anakhala pa makina othandiza kupuma kwa zaka 37 komabe anathandiza anthu 17 kudziŵa zolondola za choonadi cha m’Baibulo siinakulimbikitseni? Mofananamo, chitsanzo chanu chingalimbikitse okhulupirira anzanu kulimbikira potumikira Yehova.—g93-E 1/22 tsa. 18-21.
5 Ngakhale ngati vuto lanu likukulepheretsani kupita mu utumiki monga mmene mumafunira, mungalimbikitsebe ena. Mbale wina anati: “Ndaona kuti ngakhale munthu wolumala kwambiri angathandize zedi anthu ena. Ine ndi mkazi wanga takhala othandiza nthaŵi zonse kwa anthu osiyanasiyana mu mpingo. Chifukwa cha vuto lathu, nthaŵi zonse sitichoka, munthu amatipeza nthaŵi iliyonse.” Komabe, chifukwa cha vuto lanu, n’zachidziŵikire kuti si nthaŵi zonse zimene mudzachita zinthu mogwirizana ndi changu chanu. Komabe, mutathandizidwa zina n’zina mungakhale achangu mu utumiki. Choncho, ngati mukufuna thandizo lililonse, musazengereze kuwauza akulu kapena anthu ena mu mpingo amene angakuthandizeni.
6 Yehova amaona zonse zimene mumachita pomutumikira, ndipo amayamikira utumiki wanu wa mtima wonse. (Sal. 139:1-4) Mukamudalira iye, adzakupatsani mphamvu kuti utumiki wanu ukhale wobala zipatso ndi watanthauzo.—2 Akor. 12:7-10.