Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/03 tsamba 1
  • Kuyamikiridwa Kumalimbikitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyamikiridwa Kumalimbikitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • “Mawu a pa Nthawi Yake Kodi Sali Abwino?”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Musaiwale Kuti M’pofunika Kwambiri Kuyamikira Ena
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayamikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuyamikira Ena?
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 11/03 tsamba 1

Kuyamikiridwa Kumalimbikitsa

1 “Kodi lero sindinali mwana wabwino?” mwana wina analankhula zimenezi akulira pa nthaŵi yogona. Funso limeneli linadabwitsa kwambiri amayi ake. Ngakhale kuti amayiwo anaona kuti mwanayo wayesetsa kusonyeza khalidwe labwino tsiku limeneli, iwo sanamuyamikire m’pang’ono pomwe. Kulira kwa mwana ameneyu kukusonyeza kuti tonsefe, ana ndi akulu, timafuna kuyamikiridwa. Kodi timalimbikitsa anthu amene timakhala nawo mwa kuwayamikira chifukwa cha zinthu zabwino zimene amachita?—Miy. 25:11.

2 Palitu zifukwa zomveka ndiponso zambiri zoyamikirira Akristu anzathu. Akulu, atumiki otumikira, ndi apainiya amagwira ntchito molimbika kuti akwaniritse maudindo awo. (1 Tim. 4:10; 5:17) Makolo oopa Mulungu amachita zonse zimene angathe kuti alere ana awo m’njira ya Yehova. (Aef. 6:4) Achinyamata achikristu amamenyera nkhondo zolimba kuti akane “mzimu wa dziko lapansi.” (1 Akor. 2:12; Aef. 2:1-3) Ena amatumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti ndi okalamba, odwala, kapena ali ndi mavuto ena. (2 Akor. 12:7) Anthu onseŵa amafunika kuwayamikira. Kodi timayamikira zinthu zabwino zimene iwo amachita?

3 Yamikirani Munthu Payekha Ndiponso Molunjika: Tonse timasangalala kwambiri kumva munthu akutiyamikira papulatifomu. Komabe, kuyamikira kumakhala kolimbikitsa kwambiri akatiuza ifeyo patokha. Mwachitsanzo, Paulo mu chaputala 16 cha kalata yake yopita kwa Aroma, ananena mawu achindunji oyamikira anthu ena monga Febe, Priska ndi Akula, Trufena ndi Trufosa, ndiponso Persida. (Aroma 16:1-4, 12) Mawu akewo ayenera kuti analimbikitsa kwambiri anthu okhulupirika ameneŵa. Kuyamikira koteroko kumatsimikizira abale ndi alongo athu kuti ndi ofunika ndipo kumatithandiza kuti tigwirizane nawo kwambiri. Kodi posachedwapa mwayamikirapo munthu payekha ndiponso molunjika?—Aef. 4:29.

4 Yamikirani Kuchokera mu Mtima: Kuti kuyamikira kwathu kukhale kolimbikitsa, kuyenera kuchokera pansi pa mtima. Anthu amadziŵa ngati tikunena zochokera pansi pa mtima kapena ngati ‘tikungosyasyalika ndi lilime.’ (Miy. 28:23) Ngati tiphunzira kuona zabwino mwa anthu ena, mtima wathu udzafuna kuwayamikira. Tiyeni tikhaletu owoloŵa manja poyamikira ena moonadi, podziŵa kuti ‘mawu a panthaŵi yake ali abwino.’—Miy. 15:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena