Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov. 15
“M’mbuyomu, anthu ambiri ankakhulupirira kuti tsiku lina dziko lapansili lidzakhala paradaiso. Masiku ano, ena akukayikira ngati lidzapitirizebe kukhalapo. Kodi maganizo anu ndi otani ponena za tsogolo la dzikoli? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zomwe Baibulo limanena pankhaniyi. [Ŵerengani Salmo 37:11.] Magazini iyi ikufotokozanso zina zomwe Baibulo linaneneratu zokhudza dziko lapansili.”
Galamukani! Nov. 8
“Kodi mwaona kuti nthaŵi zambiri tikumva za tizilombo toyambitsa matenda tokana mankhwala? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikupenda zimene zikupangitsa zimenezi ndipo ikutchula zina zimene tingachite kuti tidziteteze. Ikufotokozanso lonjezo la m’Baibulo la dziko limene simudzakhala munthu aliyense wodwala.” Ŵerengani Yesaya 33:24.
Nsanja ya Olonda Dec. 1
“Anthu ena masiku ano akusiya kukhulupirira Mulungu. Chifukwa chimodzi chomwe akuchitira zimenezi n’chakuti sakupeza mayankho ogwira mtima a mafunso ovutitsa maganizo monga aŵa. [Perekani chitsanzo kuchokera m’bokosi la patsamba 6.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza mfundo imodzi yofunika kwambiri kuti munthu ukhale ndi chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu.” Ŵerengani Afilipi 1:9.
Galamukani! Nov. 8
“Zinthu zopangidwa kuchokera ku mafuta okumbidwa pansi zimakhudza pafupifupi mbali zonse za moyo wathu. Kodi munayamba mwaganizapo mmene moyo ungakhalire popanda zinthu zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zinachititsa kuti mafuta akhale ofunika kwambiri kwa anthu masiku ano. Ikufotokozanso chifukwa chimene sitiyenera kudera nkhaŵa kuti tsiku lina mafutaŵa adzatha.”