Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2004
1 Yehova akuthandiza anthu wamba kuti akwaniritse ntchito yofunika kwambiri padziko lonse. Njira imodzi yomwe akuchitira zimenezi ndiyo kudzera m’maphunziro operekedwa mlungu uliwonse m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kodi mumatenga nawo mbali mokwanira monga momwe mungathere? Mu January chaka chamaŵa, padzakhala kusintha pang’ono n’cholinga chothandiza ophunzira kupindula nayo kwambiri sukuluyi.
2 Kusinthasintha Mlangizi Wothandiza: Abale amene amakamba nkhani zolangiza ndi mfundo zazikulu za Baibulo akhala akuyamikira kwambiri malangizo a mlangizi wothandiza. M’mipingo yomwe muli akulu ambiri odziŵa kuphunzitsa, angathe kumasintha mlangizi wothandiza chaka chilichonse. Kuchita zimenezi kungapangitse kuti azithandizana ntchitoyi; komanso chomwe chingakhale chothandiza kwambiri n’chakuti akulu ndi atumiki otumikira oyenerera bwino angapindule ndi nzeru zomwe angapeze kwa anthu osiyanasiyana odziŵa bwino kukamba nkhani ndiponso kuphunzitsa.
3 Kusintha Tsiku la Kubwereza kwa Pakamwa: Ngati mpingo wanu uli ndi msonkhano wadera mlungu wa kubwereza kwa pakamwa, ndiye kuti kubwerezaku (pamodzi ndi ndandanda yonse ya mlungu wa kubwerezawo) kuzichitika mlungu wotsatira pambuyo pa msonkhano waderawo. Ndipo ndandanda ya mlungu wa kutsogolowo, iyenera kuchitidwa pa mlungu wa msonkhano waderawo. Komabe, kusintha kotereku sikuyenera kuchitika ngati woyang’anira dera akuchezera mpingo wanu mlungu wa kubwereza kwa pakamwa. M’malo mwake muyenera kukhala ndi nyimbo, luso la kulankhula, ndi mfundo zazikulu za Baibulo za mlunguwo. Ndipo nkhani yolangiza (yomwe imakambidwa pambuyo pa luso la kulankhula) iyenera kutengedwa pa ndandanda ya mlungu wotsatira. Mfundo zazikulu za Baibulo ziyenera kutsatiridwa ndi Msonkhano wa Utumiki wa mphindi 30, womwe ungasinthidwe n’kukhala ndi mbali zitatu za mphindi 10 iliyonse kapena mbali ziŵiri, iliyonse ya mphindi 15. (Pasakhale zilengezo zotsegulira.) Msonkhano wa Utumiki ukatha, payenera kuimbidwa nyimbo woyang’anira dera asanakambe nkhani yake ya mphindi 30. Ndiyeno mlungu wotsatira, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu izikhala ndi luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za Baibulo monga mmene zilili pa ndandanda kenako kubwereza kwa pakamwa.
4 Tengeranipo mwayi pa mpata uliwonse wokuthandizani kuti mukule mwauzimu. Pamene mukupindula ndi maphunziro anu a m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, mumalimbikitsa mpingo wanu, mumatengamo mbali n’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, ndiponso mumatamanda Mlembi wa uthenga wabwino umene timalalikira.—Yes. 32:3, 4; Chiv. 9:19.