Kupezeka Pamisonkhano Nthaŵi Zonse Kukhale Patsogolo
1 Mabanja achikristu amaika patsogolo kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Koma zimene moyo umafuna masiku ano zingavutitse zinthu. Kodi ntchito za pakhomo, ntchito yolembedwa, kapena homuweki, zayamba kudya nthaŵi ya kulambira Yehova? Kuona zinthu mogwirizana ndi “maganizo” a Yehova kudzatithandiza kuika patsogolo zinthu zofunika.—1 Sam. 24:6; 26:11, NW.
2 Mwa kutola nkhuni tsiku la Sabata, mwamuna wina wachiisrayeli analephera dala kuona zinthu mmene Yehova amaonera. Mwina iye anaganiza kuti kuchita zimenezo kunali kusamala banja lake; mwinanso anaona ngati imeneyo sinali nkhani yaikulu. Koma ndi chiweruzo chimene chinaperekedwa, Yehova anasonyeza kuti kuchita ntchito za masiku onse pa nthaŵi ya kulambira ndi mlandu waukulu zedi.—Num. 15:32-36.
3 Kuthana ndi Vutolo: Kwa ambiri ndi nkhondo kuti aonetsetse kuti ntchito yawo yolembedwa sikuwalepheretsa kupezeka pamisonkhano. Ena athana ndi vutoli mwa kukambirana ndi owalemba ntchito, kusinthana mashifiti ndi anzawo akuntchito, kupeza ntchito ina yowapatsa mpata, kapena kusintha zina n’zina pa moyo wawo kuti asamafune zambiri. Kunena zoona, nsembe zotero pa kulambira koona zimakondweretsa Mulungu.—Aheb. 13:16.
4 Homuweki ingakhalenso vuto. “Ndimayamba kulemba homuweki tisanapite ku misonkhano ndipo ndimadzamaliza tikabwerako,” anatero mtsikana wina. Ngati ana awo sanathe kumaliza homuweki tsiku la msonkhano, makolo ena apita kwa aphunzitsi kukawafotokozera kuti kwa iwo ndi banja lawo kupezeka pamisonkhano yachikristu ndiko chinthu choyamba.
5 Ngati pabanja pali dongosolo labwino ndipo amagwirizana, zimathandiza kumaliza ntchito za pakhomo mwamsanga pokonzekera kuti banja lonse likapezeke kumsonkhano panthaŵi yake. (Miy. 20:18) Ngakhale ana aang’ono angaphunzitsidwe kuvala ndi kukonzekera kupita ku msonkhano panthaŵi yoikika. Mwa kupereka chitsanzo chabwino, makolo angatsindike kwa ana awo mfundo yakuti misonkhano n’njofunika kwambiri.—Miy. 20:7.
6 Pamene mavuto m’dzikoli akuwonjezeka, m’pofunika kuti tizipezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Tipitirizetu kuona zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova ndi kuonetsetsa kuti kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse kuli patsogolo.—Aheb. 10:24, 25.