Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova
1 Pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Olengeza Ufumu Achangu,” tinasangalala kulandira buku la Yandikirani kwa Yehova. Ambiri anaŵerenga bukuli atangolandira. Mosakayika, enanso ambiri analimbikitsidwa kuŵerenga chifukwa cha lemba la chaka cha 2003 lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yak. 4:8.
2 Mwezi wa March tidzayamba kuphunzira buku la Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Buku la Mpingo. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapindule kwambiri ndi phunzirolo? M’pofunika kukonzekera. Mutu uliwonse udzatenga milungu iŵiri, ndipo akonza zophunzira ndime zoŵerengeka chabe mlungu uliwonse. Zimenezi zidzakupatsani mpata wopereka ndemanga zochokera pansi pa mtima zimene munapeza pophunzira ndi posinkhasinkha nkhaniyo. Ndiponso, m’milungu imene tizikambirana mbali yomaliza ya mutu tizipenda ndime zocheperapo kuti tikhale ndi nthaŵi yogwiritsa ntchito mbali yapadera ya bukuli.
3 Kuyambira mutu 2, chakumapeto kwa mutu uliwonse kuli bokosi la mutu wakuti “Mafunso Owasinkhasinkha.” Atamaliza kukambirana ndime yomaliza m’mutu uliwonsewo, woyang’anira phunziro la buku adzakambirana ndi kagulu kake za m’bokosilo. Adzawalimbikitsa kupereka ndemanga zawo, kutchula mfundo zabwino zimene anapeza posinkhasinkha Malembawo. (Miy. 20:5) Kuwonjezera pa mafunso amene ali m’bokosimo, iye nthaŵi zina angafunse mafunso onga akuti: “Kodi zimenezi zikukuuzani chiyani za Yehova? Kodi zikukhudza motani moyo wanu? Kodi mungazigwiritse ntchito motani kuthandizira ena?” Cholinga chake chidzakhale kuwalimbikitsa kupereka ndemanga zochokera pansi pa mtima, osati kuwayesa nzeru pa mfundo zosafunika kwenikweni.
4 Buku la Yandikirani kwa Yehova n’losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse. Inde, mabuku onse a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amalemekeza Yehova, koma buku ili lakonzedwa ndi cholinga chofotokoza makhalidwe a Yehova basi. (Mat. 24:45-47) Komatu ndiye tikuyembekeza kudzasangalala! Tidzapindula kwambiri pophunzira mwakuya za umunthu wa Yehova. Phunziro limeneli lidzatithandizetu kuyandikira kwambiri kwa Atate wathu wa kumwamba, ndipo tidzakhaletu ogwira mtima pothandiza ena kuchita chimodzimodzi.