Nkhondo ya Apakavalo Imene Mukumenya Nawo
1, 2. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano akuthandiza bwanji kukwaniritsa masomphenya aulosi opezeka pa Chivumbulutso 9:13-19?
1 ‘Mngelo wachisanu ndi chimodzi anawomba lipenga lake.’ Kenako, ‘ankhondo apakavalo’ okwana “zikwi makumi aŵiri zochulukitsa zikwi khumi” anachita phokoso langati bingu. Limeneli si gulu la ankhondo wamba. “Mitu ya akavalo [ili] ngati mitu ya mikango.” Mkamwa mwawo mukutuluka moto, utsi, ndi sulfure ndipo “michira yawo ifanana ndi njoka.” N’chifukwa chake gulu la ankhondo lophiphiritsira limeneli lasakaza kwambiri. (Chiv. 9:13-19) Kodi mukudziŵa mmene mukuthandizira pokwaniritsa masomphenya aulosi wapadera umenewu?
2 Otsalira odzozedwa ndi anzawo, a nkhosa zina, amalengeza ziŵeruzo za Mulungu mogwirizana. Zimenezi zachititsa kuti Matchalitchi Achikristu aonekere poyera kuti ndi akufa mwauzimu. Tiyeni tipende mbali ziŵiri za masomphenya aulosi zimene zikusonyeza chifukwa chake ntchito ya atumiki a Mulungu ikuyenda bwino kwambiri.
3. Kodi mwaphunzitsidwa bwanji kuti mulankhule uthenga wa Mulungu mogwira mtima?
3 Ophunzitsidwa Ndiponso Okonzeka Kupereka Uthenga wa Mulungu: Mwa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndiponso misonkhano ina yampingo, atumiki a Mulungu aphunzitsidwa kulankhula uthenga wa Mulungu mogwira mtima. Potsanzira Yesu ndi ophunzira ake, iwo amapita kukafunafuna anthu oyenera, amalalikira kulikonse kumene angapeze anthu. (Mat. 10:11; Marko 1:16; Luka 4:15; Mac. 20:18-20) Njira yopezeka m’Baibulo yochitira ulaliki imeneyi yakhala yothandiza kwambiri.
4. Ndi zida ziti zimene ofalitsa ambiri ali nazo zowathandiza pogwira ntchito yawo?
4 Atumiki achikristu agaŵira mamiliyoni ambiri a Mabaibulo, mabuku, mabulosha, ndiponso magazini pogwira ntchito ya Mulungu yolalikira. Zofalitsa zimenezi zilipo m’zinenero pafupifupi 400, zokhudza nkhani zambiri zosiyanasiyana ndiponso zolembedwa mosangalatsa anthu osiyanasiyana. Kodi mumagwiritsa ntchito bwino zida zimenezi?
5, 6. N’chiyani chimasonyeza kuti anthu a Yehova amathandizidwa ndi Mulungu?
5 Utsogoleri Ndiponso Thandizo Lochokera Kumwamba: Masomphenya aulosiwa akusonyezanso bwino kuti ntchito imene ankhondo apakavalo akuphiphiritsira imathandizidwa ndi Mulungu. (Chiv. 9:13-15) Ntchito yolalikira yapadziko lonse ikuchitika mwa mzimu wa Mulungu osati mwa nzeru kapena mphamvu za anthu. (Zek. 4:6) Yehova akugwiritsa ntchito angelo kutsogolera ntchito imeneyi. (Chiv. 14:6) Chotero, kuphatikiza pantchito imene Mboni zake zikugwira, Yehova akupereka thandizo lochokera kumwamba kuti akokere anthu ofatsa kwa iye.—Yoh. 6:45, 65.
6 Chifukwa chakuti anthu a Yehova aphunzitsidwa, akonzekera bwino kupereka uthenga wa Mulungu, ndiponso akugwira ntchito motsogoleredwa ndi angelo, ntchito yawo singaimitsidwe. Choncho tiyeni tipitirize kuchita mbali yathu pokwaniritsa masomphenya aulosi osangalatsa ameneŵa.