Khalani Oyera m’Makhalidwe Anu Onse
1. N’chifukwa chiyani n’kofunika kukhala oyera m’makhalidwe athu onse?
1 Monga atumiki a Mulungu woyera, Yehova, timayesetsa kukhala oyera m’makhalidwe athu onse. (1 Pet. 1:15, 16) Izi zikutanthauza kuti timayesetsa kutsatira miyezo ya Yehova m’mbali zonse za moyo wathu. Msonkhano wachigawo wa chaka chino utipatsa mpata wapadera wosonyeza khalidwe loyera.
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuganizira ena pamene tikudya ku lesitilanti?
2 Ku Lesitilanti: Woperekera zakudya pa lesitilanti yapafupi ndi malo amsonkhano wina anati: “Mboni n’zosiyana ndi anthu ena. Zimalemekeza anthu ena.” Khalidwe labwino limaphatikizapo kusalankhula ndiponso kuseka mokuwa kumene kungasokoneze ena amene akudya. Ngakhale pamene tikudya ndi kumwa, timafuna kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.—1 Akor. 10:31.
3. Kodi khalidwe labwino pamalo amsonkhano likuphatikizapo kuchita chiyani?
3 Pamsonkhano: Khalidwe labwino liyenera kuonekera makamaka pamalo amsonkhano. Chonde mverani malangizo a akalinde, kaya ndi koimika magalimoto kapena mu holo. (Aheb. 13:17) Mabanja ayenera kukhala pamodzi osati kusiya ana awo, ndi achinyamata a zaka zapakati pa 13 mpaka 19, kukhala m’timagulu ndi achinyamata anzawo. Musalumikize makina aliwonse ojambulira ku magetsi kapena ku zokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muwagwiritse ntchito popanda kudodometsa nawo ena. Ngati mukufuna kujambula zithunzi mapulogalamu ali m’kati, musagwiritse ntchito fulashi. Matelefoni a m’manja achunidwe moti asadodometse ena. Mukaona kuti pachitika ngozi pamalowo, chonde dziŵitsani akalinde kapena Dipatimenti ya Chipatala. Pamakhala anthu odziŵa ntchito yachipatala pamalo amsonkhano omwe angathandize.
4. Kodi khalidwe lathu pamisonkhano yachigawo limalemekeza bwanji Mulungu?
4 Khalidwe lathu limatisiyanitsa ndi anthu ena ndiponso limalemekeza Mulungu wathu. (1 Pet. 2:12) Pamalo amsonkhano, zochita za Mboni za Yehova zidzakhala pachionetsero. Choncho, tsimikizani mtima kukhala oyera m’makhalidwe anu onse.
[Bokosi patsamba 5]
Sonyezani Khalidwe Loyera
◼ Yang’anirani kwambiri ana anu
◼ Ganizirani ena