Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/04 tsamba 4
  • Gwiritsani Ntchito Bwino Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwiritsani Ntchito Bwino Baibulo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukuchita Utumiki Wanu Mokwanira?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 3:
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Kutchula Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 9/04 tsamba 4

Gwiritsani Ntchito Bwino Baibulo

1. Kodi muyenera kuchita chiyani mukamakonzekera utumiki wa kumunda?

1 Kaya ndi buku lanji limene takonzekera kukagaŵira mu utumiki, zimakhala zopindulitsa kwambiri kusankha lemba limene lingam’pangitse munthu kuganiza loti tikakambirane ndi amene akamvetsere. (Aheb. 4:12) Kusankha lemba limene aligwiritsa ntchito m’buku limene mukugaŵira kumapangitsa kuti zisakuvuteni kugaŵira bukulo. M’madera ena, ofalitsa aona kuti zimawathandiza kwambiri kunyamula Baibulo m’manja akamayandikira munthu kapena akamachita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba.

2. (a) Kodi tingayambitse motani kukambirana pogwiritsa ntchito lemba? (b) Kodi ndi nkhani ziti za m’Malemba zimene zimasangalatsa anthu m’gawo lanu?

2 Yambani ndi Lemba: Ofalitsa ena amayamba ulaliki wawo mwa kum’funsa mwininyumba funso losavuta loti afotokoze maganizo ake pa lemba linalake la m’Baibulo, ndiyeno amaŵerenga lembalo. Funsolo limachititsa munthuyo kuti akhale ndi chidwi ndi Mawu a Mulungu. Kodi mawu ena mwa mawu otsatiraŵa angakhale othandiza m’gawo lanu kuyambira kukambirana?

◼ “Mukanakhala ndi mphamvu yochitira zimene akunena pa lembali, kodi mukanasintha zinthu?” Ŵerengani Chivumbulutso 21:4.

◼ “N’chifukwa chiyani tikukhala m’nthaŵi zovuta ngati zimenezi?” Ŵerengani 2 Timoteo 3:1-5.

◼ “Kodi mukuganiza kuti dera lathu lino likanakhala malo abwino ngati munthu aliyense akanatsatira langizo ili?” Ŵerengani Mateyu 7:12.

◼ “Kodi mukuganiza kuti ana anu adzatha kusangalala ndi moyo wabwino ngati umene akufotokoza apawu?” Ŵerengani Salmo 37:10, 11.

◼ “Kodi mukuganiza kuti tsiku lina mawu aŵa adzakwaniritsidwa?” Ŵerengani Yesaya 33:24.

◼ “Kodi kusintha kwa boma kumene akukutchula apa mumakudziŵa bwinobwino?” Ŵerengani Danieli 2:44.

◼ “Kodi munaganizapo nthaŵi inayake zofunsa Mulungu funso ili?” Ŵerengani Yobu 21:7.

◼ “Kodi n’zotheka kudzaonanso okondedwa athu amene anamwalira?” Ŵerengani Yohane 5:28, 29.

◼ “Kodi akufa amadziŵa zimene amoyo akuchita?” Ŵerengani Mlaliki 9:5.

3. Kodi tingawathandize motani anthu kumvetsetsa mawu amene tawaŵerengera m’Baibulo?

3 Kufotokoza, Kuchitira Fanizo, Kugwirizanitsa: Ngati munthu akufuna kuti mukambirane naye, musakambirane naye mothamanga. Khalani ndi nthaŵi yokwanira yom’fotokozera bwinobwino, chitirani fanizo, ndipo gwirizanitsani fanizolo ndi lemba limene mwaliŵerenga kuti munthuyo athe kulimvetsetsa. (Neh. 8:8) Anthu akamvetsetsa ndi kuvomereza zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa, moyo wawo ungasinthe modabwitsa kwambiri.—1 Ates. 2:13.

4. Kodi tingagwiritse ntchito bwino bwanji Baibulo pa ulendo wobwereza?

4 Pitirizani kugwiritsa ntchito bwino Baibulo pamene mukukulitsa chidwi chimene anthu ali nacho. Mungathe kugwiritsa ntchito njira yomweyi pamene mukupanga maulendo obwereza: (1) Sankhani lemba loyenerera. (2) Funsani funso losavuta lofuna kuti afotokoze maganizo ake pa lemba linalake. Ndiyeno ŵerengani lembalo. (3) Lifotokozeni, chitirani fanizo, ndipo ligwirizanitseni ndi nkhaniyo. Yesetsani kuthandiza munthuyo kuwonjezera zimene akudziŵa pa Mawu a Mulungu nthaŵi iliyonse imene mwapitako. Posapita nthaŵi, mungayambe kuchititsa phunziro la Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena