Pitirizanibe Kukhala Achangu!
1 Yesu ankadziŵa kuti nthaŵi imene anali nayo yoti achite ntchito ya Atate wake pano padziko lapansi inali yochepa. (Yoh. 9:4) Pachifukwa chimenechi, iye anachita utumiki wake mwachangu, ndipo anaphunzitsanso ophunzira ake kuchitanso chimodzimodzi. (Luka 4:42-44; 8:1; 10:2-4) Kwa iye zinthu zosamalira moyo zinali pamalo achiŵiri. (Mat. 8:20) N’chifukwa chake anakwanitsa kumaliza ntchito imene Yehova anam’patsa kuti aichite.—Yoh. 17:4.
2 Nthaŵi ndi Yochepa: Nthaŵi yoti tilalikire uthenga wabwino “padziko lonse lapansi” ilinso yochepa. (Mat. 24:14) Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti tikukhala m’kati mwenimweni mwa nthaŵi ya mapeto. Posachedwapa “iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu . . . adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Ates. 1:6-9) Chiweruzo chimenechi chidzafika modzidzimutsa kwambiri. (Luka 21:34, 35; 1 Ates. 5:2, 3) Anthu afunika kudziŵa ngozi imene alipo. Choncho ndi udindo wathu kuwathandiza kuti adziŵe Yehova nthaŵi idakalipo kotero kuti awakomere mtima.—Zef. 2:2, 3.
3 Kuchita Zonse Zimene Tingathe: Pozindikira kuti “yafupika nthaŵi,” atumiki a Mulungu amaika patsogolo ntchito yolalikira. (1 Akor. 7:29-31; Mat. 6:33) Ena asankha kusiya kuchita zinthu zina zomwe zikanawapezetsa chuma chochuluka kapena kusiya zochita zina zaumwini n’cholinga chofuna kuwonjezera utumiki wawo. (Marko 10:29, 30) Ena akupitirizabe kukhala ‘ochuluka mu ntchito ya Ambuye’ ngakhale kuti akupirira ziyeso zosatha. (1 Akor. 15:58) Ambiri akhala akulalikira uthenga wabwino kwa zaka zambiri popanda kubwerera m’mbuyo. (Aheb. 10:23) Yehova amaona kudzipereka koteroko kofuna kuchirikiza zinthu za Ufumu kukhala kwa mtengo wapatali.—Aheb. 6:10.
4 Kuika moyo wathu pa kulambira Yehova, kumene kumaphatikizapo ntchito yolalikira, kumatithandiza kuti m’maganizo mwathu tizikumbukira za kuyandikira kwa tsiku la Yehova. Kumatiteteza kuti dziko la Satanali lisatisokoneze ndiponso timalimbikira kukhalabe ndi khalidwe loyera. (2 Pet. 3:11-14) Ndithudi, kuchita utumiki wathu mwachangu kungakhale kopulumutsa moyo wathu ndi wa iwo amene angatimvetsere.—1 Tim. 4:16.