Thandizo Lanu Likufunika
1 “Zikomo kwambiri chifukwa cha zonse zimene mumatichitira. Mumatithandiza kwambiri.” Ndemanga imeneyi ikusonyeza bwino mmene timayamikira akulu ndi atumiki otumikira. Popeza kuti gulu la Mulungu likupitirizabe kukula, pakufunika amuna okhwima mwauzimu kuti atumikire m’mipingo pafupifupi 100,000 imene ili padziko lonse. Ngati ndinu mbale wobatizidwa, thandizo lanu likufunika.
2 Kukalamira Udindo: Kodi muyenera kuchita chiyani pokalamira maudindo owonjezereka? (1 Tim. 3:1) Mwachidule, tinganene kuti muyenera kuonetsa chitsanzo chabwino m’mbali zonse za moyo wanu. (1 Tim. 4:12; Tito 2:6-8; 1 Pet. 5:3) Muzitenga nawo mbali mokwanira mu ntchito yolalikira ndi kuthandiza ena kuchitanso zomwezo. (2 Tim. 4:5) Muziganizira kwambiri okhulupirira anzanu. (Aroma 12:13) Muziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kuyesetsa kukhala ndi luso la kuphunzitsa. (Tito 1:9; 1 Tim. 4:13) Ntchito iliyonse imene akulu angakupatseni muziichita mwakhama. (1 Tim. 3:10) Ngati ndinu mutu wa banja, ‘muziweruza bwino nyumba yanu.’—1 Tim. 3:4, 5, 12.
3 Kutumikira pa udindo winawake ndi ntchito yaikulu ndipo imafuna mzimu wodzipereka. (1 Tim. 5:17) Choncho, pokalamira udindo yesetsani kutumikira ena modzichepetsa. (Mat. 20:25-28; Yoh. 13:3-5, 12-17) Sinkhasinkhani za mtima umene Timoteo anali nawo ndipo yesetsani kum’tsanzira. (Afil. 2:20-22) Mofanana ndi iye, yesetsani kukhala ndi mbiri yabwino posonyeza khalidwe labwino. (Mac. 16:1, 2) Mukamayesetsa kukhala ndi makhalidwe auzimu ofunika kuti musamalire maudindo owonjezereka ndiponso mukamagwiritsa ntchito malangizo okuwongolerani amene ena angakupatseni, kupita patsogolo kwanu kudzaonekera kwa anthu onse.—1 Tim. 4:15.
4 Makolo, Phunzitsani Ana Anu Kuthandiza: Ana akhoza kuphunzira kukhala othandiza kuyamba adakali aang’ono. Aphunzitseni kukhala tcheru pamisonkhano, kulalikira, ndi kukhala ndi khalidwe labwino pa Nyumba ya Ufumu ndi kusukulu. Aphunzitseni kuti azikonda kutumikira ena, kuchita zinthu monga kuthandiza nawo kuyeretsa pa Nyumba ya Ufumu, kuthandiza okalamba, ndi ntchito zina. Aloleni kudzionera okha kuti ngati ali ndi mtima wopatsa adzapeza chimwemwe. (Mac. 20:35) Akaphunzitsidwa zinthu ngati zimenezi, zidzawathandiza kudzakhala apainiya, atumiki otumikira, ndi akulu m’tsogolo muno.