Bokosi la Mafunso
◼ Kodi njira yabwino yoperekera ndalama zothandizira abale amene akufunika thandizo m’mayiko ena ndi iti?
Nthawi zina, timamva za abale a m’mayiko ena amene akufunika thandizo la zinthu zakuthupi chifukwa chokumana ndi chizunzo, tsoka, kapena mavuto ena. Abale ena mwa kufuna kwawo atumiza ndalama mwachindunji ku maofesi a nthambi a kumayiko kumene kukufunika chithandizoko n’kupempha kuti ndalamazo zigwiritsidwe ntchito kuthandizira munthu winawake, mpingo winawake, kapena ntchito ina ya zomangamanga.—2 Akor. 8:1-4.
Popeza kuti kudera nkhawa okhulupirira anzathu koteroko n’koyamikirika, nthawi zambiri pamakhala zinthu zina zofunika thandizo la mwamsanga losiyana ndi zimene wothandizayo ali nazo m’maganizo. Nthawi zina zimachitika kuti vuto limene linalipolo lasamaliridwa kale. Ngakhale zitero, ngati tatumiza ndalama zathu ku ofesi ya nthambi kaya zikhale za ntchito ya padziko lonse, za Thumba la Nyumba za Ufumu, kapena zothandizira pakagwa tsoka, timakhala ndi chikhulupiriro kuti zoperekazo zidzagwiritsidwa ntchito mogwirizana ndi mmene woperekayo wanenera.
Abale a m’nthambi zonse ndi ophunzitsidwa bwino kuti azichitapo kanthu mwamsanga pakafunika thandizo la mwadzidzidzi. Mulimonse mmene zingakhalire, nthambi imadziwitsa Bungwe Lolamulira za zimenezi. Ngati pakufunika thandizo lina, Bungwe Lolamulira limapempha nthambi za kufupi ndi kumene kukufunikira thandizoko kuti zithandize ndipo nthawi zina ndalama zimatha kuchokera komwe ku likulu.—2 Akor. 8:14, 15.
Choncho, zopereka zonse zothandizira ntchito ya padziko lonse, ntchito ya zomangamanga m’mayiko ena, kapena zothandizira pakagwa tsoka ziyenera kuperekedwa ku ofesi ya nthambi ya dziko limene mukukhala, mwina kudzera ku mpingo kapena kuzipereka mwachindunji ku ofesi ya nthambi. Mwanjira imeneyi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kudzera m’makonzedwe a gulu okhazikitsidwa ndi Bungwe Lolamulira, amasamalira zosowa za gulu lonse la abale padziko lonse mwadongosolo.—Mat. 24:45-47; 1 Akor. 14:33, 40.