Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 15
“Tonse timafuna moyo wabwino, wathu ndi wa ana athu. Koma ambiri amaona kuti sangaupeze. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka ife kusintha tsogolo lathu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikutisonyeza kuchokera m’Baibulo kuti tingakwanitse kutero, ndi kuti tsogolo lathu likudalira zimene tingasankhe panopa.” Werengani Deuteronomo 30:19.
Galamukani! Feb. 8
“Tonsefe tikadwala, timayamikira dokotala amene amatimvetsetsa mmene tikumvera. Koma kodi mukuganiza kuti odwala ambiri amayamba aganiza kaye za mmene madokotala awo amamvera? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto amene madokotala akukumana nawo ndiponso tsogolo lake la sayansi ya zamankhwala.” Werengani Yesaya 33:24.
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Kodi sizikupwetekani kuti masiku ano anthu ambiri akuponderezedwa ndi kuchitidwa nkhanza? [Tchulani nkhani ya posachedwapa imene ambiri akuidziwa m’deralo, ndipo yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Mulungu amaonera moyo wa anthu. Ikufotokozanso mmene adzatipulumutsire ku mavuto amene alipowa.” Werengani Salmo 72:12-14.
Galamukani! Feb. 8
“Masiku ano, mwa mavuto akuluakulu amene timakumana nawo, limodzi mwa mavutowo ndi kupanikizika. Kodi si zoona zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo linaneneratu molondola kuti zimenezi zidzachitika. [Werengani 2 Timoteo 3:1.] Magazini iyi ili ndi mfundo zabwino kwambiri zimene zingakuthandizeni inuyo ndi banja lanu kupirira mukapanikizika.”