Yamikani Yehova mu Msonkhano Waukulu
1, 2. Kodi msonkhano wachigawo umatipatsa mpata wotani, ndipo kodi njira imodzi imene tingachitire zimenezo ndi iti?
1 Chaka chilichonse misonkhano yachigawo imatipatsa mpata wabwino wotamanda Yehova. Timamva ngati mmene anamvera Davide amene anaimba kuti: “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” (Sal. 35:18) Pa Msonkhano Wachigawo umene ukubwerawu wakuti “Kumvera Mulungu,” kodi tingatani kuti tisonyeze kuti timatamanda Yehova monga anthu ogwirizana?
2 Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo mwa khalidwe lathu. Akuluakulu oyang’anira malo ena ochitira msonkhano anati: “Malinga ndi mmene taonera misonkhano yanu, tauza magulu ena onse azipembedzo ofuna kubwereka malo athu kuti abwere kudzaona mmene Mboni za Yehova zimachitira msonkhano, chifukwa zimakhala ndi dongosolo labwino.” Chifukwa cha kaonekedwe kathu, kugwirizanika kwathu, ndi khalidwe lathu, aliyense wa ife amathandizira kuti ndemanga zoyamikira zimenezi zikhalepo, zimene moyenerera zimapita kwa Mulungu wathu.—1 Pet. 2:12.
3, 4. Kodi kudzichepetsa kudzatithandiza bwanji kuti tivale zoyenera atumiki achikristu, pamene tili pamsonkhano ndiponso msonkhano ukatha tsiku lililonse?
3 Kaonekedwe Kathu: Kuti tivale ndi kudzikongoletsa m’njira imene imalemekeza Yehova, pamafunika kudzichepetsa. (1 Tim. 2:9) Buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 132, limati: “Munthu wodzichepetsa amapewa kukhumudwitsa ena popanda chifukwa. Amapewanso kudzionetsera.” M’mayiko ambiri, kuvala kopanda ulemu n’kofala kwambiri. Koma Yehova amayamikira kwambiri kuyesetsa kwathu kumuimira m’njira yoyenera. (Mac. 15:14) Ngakhale kuti msonkhano ungachitikire m’bwalo la masewera kapena malo osangalalira, tikasonkhana choncho timakhala tili pa “msonkhano waukulu” wa mpingo kwa masiku onse atatu a msonkhanowo. Choncho, pamene tikusonkhana pamaso pa Yehova, tiyenera kuvala mwaulemu, moyenerana ndi iyeyo. Tiyenera kuvala choncho chifukwa Yehova ndi Munthu wolemekezeka koposa m’chilengedwe chonse.—1 Mbiri 29:11.
4 Tikamaliza chigawo cha msonkhano tsiku lililonse, tionetsetse kuti tikuoneka bwino. Ngakhale kuti tingafune kuvala zovala wamba pa nthawi imene tikungokhala, kapena pamene tikudya pa lesitilanti, ndi bwino kuti kavalidwe kathu ndi mmene tadzikongoletsera zikhale zogwirizana ndi za anthu amene ‘amalemekeza Mulungu.’ (1 Tim. 2:10) Kavalidwe koyenera sikuti mungakadziwe poonera mavalidwe amene ali otchuka m’dzikoli. (1 Yoh. 2:16, 17) Mabuku athu achikristu ali ndi zitsanzo zabwino za amuna ndi akazi ovala mwaulemu ndiponso mwaudongo mogwirizana ndi zimene akuchita panthawiyo. Kuvala baji yathu pamene tili m’dera limene kukuchitikira msonkhanowo kudzatithandiza kukumbukira kuti ndife atumiki achikristu panthawi iliyonse.—2 Akor. 6:3, 4.
5, 6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza gome lauzimu la Yehova?
5 Lemekezani Gome la Yehova: Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse watikonzera phwando. (Yes. 25:6; 1 Akor. 10:21) Ngati timayamikiradi mwayi wathu wopezeka pa gome lauzimu la Yehova, ndiye kuti tidzakhala ndi cholinga chokapezeka kumsonkhano masiku onse atatu. Kodi mwakonza kale za malo ogona, mayendedwe, ndiponso kupempha tchuthi ku ntchito? Kodi mwapeza nthawi yokwanira bwino yokonzekera ndi yoyendera kuti mukafike mofulumira kumalo a msonkhano ndi kukakhala ndi nthawi yopeza malo, yocheza ndi abale, ndiponso kutamanda nawo Yehova mwa kuimba nyimbo yotsegulira limodzi ndi pemphero?—Sal. 147:1.
6 Kulemekeza gome la Yehova kudzatithandiza kukakhala tcheru kwambiri pa msonkhanowo ndi kupewa kulankhulalankhula ndi ena, kudya, kapena kuyendayenda pulogalamu ili m’kati. Kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yehova akupereka chakudya chauzimu chimene tikufunikira panopa. (Mat. 24:45) Palibe amene angafune kuchiphonya m’pang’ono pomwe. Makolo ayenera kukhala limodzi ndi ana awo ndi kuwathandiza kuti apindule mokwanira.—Deut. 31:12.
7. Kodi tikupemphedwa kutani pankhani ya chakudya cha masana, ndipo n’chifukwa chiyani?
7 Tikupemphedwa kutenga chakudya cha masana m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Tikuyamikira kuti ambiri anatsatira mosamala langizoli pamsonkhano wa chaka chatha. Tidzayamikira kwambiri ngati aliyense adzachitanso chimodzimodzi chaka chino. (Aheb. 13:17) Zimenezi zimapereka mpata wabwino wocheza ndi kulimbikitsana ndi abale athu ndiponso zimalimbitsa umodzi ndi mtendere, zimene zimapereka ulemerero kwa Yehova.—Sal. 133:1.
8, 9. Kodi msonkhano wachigawo umatipatsa mpata wina uti wolemekezera Yehova?
8 Kulalikira Mwamwayi: Popita ndi pobwerako ku msonkhano, timakhala ndi mipata yabwino yolemekezera Yehova ndi milomo yathu. (Aheb. 13:15) Kaya tikudya mu lesitilanti kapena tikukambirana ndi ogwira ntchito mu hotela, tiyeni tiyesetse kupeza njira zoti tiwalalikire. Maganizo ndi mitima yathu idzakhala yodzala ndi zinthu zauzimu zimene taphunzira ku msonkhano. Tiyeni tidzauzeko anthu amene tingakumane nawo mwamwayi zinthu zabwino zimenezi.—1 Pet. 3:15.
9 Tikudikirira ndi chidwi chachikulu mpata umenewu wolemekeza Yehova “m’masonkhano.” (Sal. 26:12) Tiyeni tonse pamodzi tidzayamike Yehova pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Kumvera Mulungu.”
[Bokosi patsamba 6]
Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo
◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Kwa masiku onse atatu, pulogalamu izidzayamba 8:30 m’mawa. Kutatsala mphindi zochepa kuti mapulogalamu a chigawo chilichonse ayambe, tcheyamani adzakhala pa pulatifomu nyimbo za Ufumu zamalimba zikuimbidwa. Panthawi imeneyi, tonse tiyenera kukhala pansi kuti pulogalamu iyambe bwinobwino. Lachisanu ndi Loweruka pulogalamu idzatha 4:05 madzulo ndipo Lamlungu pulogalamu idzatha 3:10 madzulo.
◼ Koimika Galimoto: Pa malo onse ochitira msonkhano padzakhala malo okwanira oimikako galimoto ndi njinga zomwe. Tikulimbikitsa onse kugwirizana ndi akalinde oyang’anira ntchito imeneyi. Eni galimoto ndi njinga ayenera kuonetsetsa kuti akhoma zitseko za galimoto ndi mawiro a njinga asanapite kukakhala.
◼ Kusunga Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.
◼ Zopereka: Pokonzekera msonkhano wachigawo pamapita ndalama zambiri. Tingasonyeze kuyamikira mwa kupereka mwaufulu pothandiza ntchito ya padziko lonse ku Nyumba ya Ufumu kapena pamsonkhano. Zopereka zonse za macheke zoperekedwa pamsonkhano wachigawo zizilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.”
◼ Amene Ali ndi Vuto la Kumva: Kumisonkhano yonse iwiri ya Chingelezi, pulogalamu idzamasuliridwa m’chinenero cha manja cha ku America. Zimenezi zidzalengezedwa poyamba chigawo choyambirira.
◼ Chakudya cha Masana: Chonde mudzabwere ndi chakudya chanu cha masana m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Chakudya chimenechi chingakhale ngati chimene ambiri amatenga panthawi yapadera ngati imeneyi, monga sangweji, tchipisi, mabisiketi kapena zipatso, mpunga, mbatata, chinangwa, mtedza wokazinga, ndi zakumwa.
◼ Kujambula: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira ku magetsi kapena ku zokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.
◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli m’kati.
◼ Mapeja ndi Foni za M’manja: Zinthu zimenezi muyenera kuzitchera kuti zisalire kuopa kusokoneza ena.
◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati munthu pamsonkhano adwala mwadzidzidzi, chonde dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzathe kuona mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.