Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 15
“Kukachitika maliro, ambiri amafuna kudziwa kuti chimene chimachitika munthu akafa n’chiyani. Kodi mukuganiza kuti tingathe kuimvetsetsa imfa? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena za anthu akufa. Ikufotokozanso zimene Mulungu walonjeza zoti adzaukitsa okondedwa athu omwe anamwalira.” Werengani Yohane 5:28, 29.
Galamukani! Sept. 8
“Kodi mwamvapo zoti pa ntchito zonse zimene zili padziko lonse lapansi ndi ntchito yokopa alendo imene ili ndi anthu ambiri koposa? [Yembekezani ayankhe.] Kuwanda kwa ntchito yokopa alendo kuli ndi ubwino wake komanso mavuto ake. Magazini iyi ikufotokoza za ubwino komanso kuipa kwa ntchito yokopa alendo yamakonoyi. Komanso ikupereka mfundo zothandiza kwa alendo okacheza kumayiko osiyanasiyana.”
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Lerolino m’dzikoli, anthu ambiri amangoyamikira khalidwe la kukhulupirika koma salitsatira. Kodi sizikanakhala bwino ngati anthu ambiri akanakhala ngati bwenzi limene alifotokoza pa lemba ili? [Werengani Miyambo 17:17. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza ubwino wokhala anthu okhulupirika m’banja lathu ndi kwa mabwenzi athu.
Galamukani! Sept. 8
“Mwina munachitapo chidwi kuona mgwirizano umene ulipo pakati pa zinthu zolengedwa. [Tchulani chitsanzo chimodzi chomwe chasonyezedwa m’nkhaniyo.] Kodi si zomvetsa chisoni kuti pakati pa anthu mgwirizano ngati umenewu ukusowa? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza za mmene Mulungu adzabweretsera mtendere ndi mgwirizano padziko lapansi.” Werengani Yesaya 11:9.