Pitirizani Kulimbikitsana
1 Mtumwi Paulo anachita zonse zomwe akanatha kulimbikitsa okhulupirira anzake. (2 Akor. 11:28, 29) Nafenso zimatikhudza abale athu akamavutika, ndipo timafuna kuwathandiza. Baibulo limasonyeza kuti aliyense, osati akulu okha, ayenera kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena. (Aroma 15:1, 2) Taganizirani njira ziwiri zimene tingasonyezere kuti tikumvera malangizo achikondi amenewa akuti, ‘limbikitsanani wina ndi mnzake.’—1 Ates. 5:11, NW.
2 Dziwani Zosowa za Ena: Mawu a Mulungu amati Dorika “anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.” (Mac. 9:36, 39) Iye ankaganizira anthu ovutika ndipo ankachita chilichonse chomwe akanatha kuwathandiza. Anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri! Nanunso mungaone kuti mbale kapena mlongo wina wokalamba akufunikira kumakamutenga popita ku misonkhano. Kapena pangakhale mpainiya amene alibe wina aliyense woti n’kumapita naye mu utumiki m’kati mwa mlungu masana. Tangoganizirani mmene mungalimbikitsire anthu amenewa ngati mutazindikira zosowa zimenezi ndi kuyesetsa kuwathandiza.
3 Kambiranani Zinthu Zauzimu: Tingathenso kulimbikitsa ena ndi nkhani zimene timalankhula. (Aef. 4:29) Mbale wina wodziwa zinthu ndithu ananenapo kuti: “Ngati mukufuna kulimbikitsa ena, lankhulani zinthu zauzimu. Kuti mulankhule zinthu zolimbikitsa, mungathe kuyamba ndi kufunsa funso losavuta lakuti, ‘Kodi munayamba bwanji choonadi?’” Asonyezeninso ana a mu mpingo mwanu kuti mumawakonda kwambiri. Thandizani anthu onse ofooka komanso amanyazi. (Miy. 12:25) Musalole kuti macheza anu angokhala a zinthu zosangalatsa za dzikoli, osakambirana ndi okhulupirira anzanu zinthu zopindulitsa zauzimu.—Aroma 1:11, 12.
4 Komabe, kodi n’chiyani kwenikweni chimene munganene kuti mulimbikitse ena? Kodi pa kuwerenga kwanu kwa Baibulo, mwawerengapo chinachake chimene chakuchititsani kuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha chikondi chake ndi kuwolowa manja kwake? Kodi mwalimbikitsidwapo ndi mfundo ina imene mwaimva pa nkhani ya onse kapena pa Phunziro la Nsanja ya Olonda? Kodi kapena mtima wanu wakhudzidwapo ndi zokumana nazo zina zolimbitsa chikhulupiriro? Ngatidi timayamikira zinthu zamtengo wapatali zauzimu zimenezi, nthawi zonse tidzakhala ndi chinachake choti tilimbikitsire nacho ena.—Miy. 2:1; Luka 6:45.
5 Mwa kuthandiza ena ndi kugwiritsa ntchito lilime lathu mwanzeru, tiyeni tipitirize kulimbikitsana wina ndi mnzake.—Miy. 12:18.