Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 8
  • Thandizani Ena Kuti Ayambe ‘Kumvera ndi Mtima’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ena Kuti Ayambe ‘Kumvera ndi Mtima’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Muli ndi “Mtima Womvera”?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Yehova Amakondwera Mukamamumvera
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Phunzirani Kumvera Mwakulandira Chilango
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 8

Thandizani Ena Kuti Ayambe ‘Kumvera ndi Mtima’

1. Kodi Yehova amafuna kuti olambira ake azichita chiyani?

1 Kumvera n’kofunikira kwambiri kuti tilambire Yehova movomerezeka. (Deut. 12:28; 1 Pet. 1:14-16) Posachedwapa, Mulungu adzapereka “chilango kwa iwo osam’dziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.” (2 Ates. 1:8) Kodi tingawathandize bwanji ena kuti ayambe ‘kumvera ndi mtima’ zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa?—Aroma 6:17.

2. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuthandiza ena kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?

2 Mwa Kuwathandiza Kukhala ndi Chikhulupiriro ndi Chikondi: M’Malemba, kumvera kumayendera limodzi ndi chikhulupiriro. Mtumwi Paulo analankhula za ‘lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere [“mwa,” NW] chikhulupiriro.’ (Aroma 16:26) Lemba la Ahebri chaputala 11 limatchula zitsanzo zambiri za anthu amene anali ndi chikhulupiriro, omwe anachita zinthu ndendende mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. (Aheb. 11:7, 8, 17) Mosiyana ndi zimenezi, kusamvera kumayendera limodzi ndi kusowa chikhulupiriro. (Yoh. 3:36; Aheb. 3:18, 19) Tifunikira kukhala ndi luso logwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti tithandize ena kukhala ndi chikhulupiriro chimene chingawathandize kumvera.—2 Tim. 2:15; Yak. 2:14, 17.

3. (a) Kodi kumvera ndi chikondi zimagwirizana bwanji? (b) Kodi ophunzira Baibulo tingawathandize bwanji kukonda Yehova?

3 Kumvera ndi kukonda Mulungu zimayenderanso limodzi. (Deut. 5:10; 11:1, 22; 30:16) Lemba la 1 Yohane 5:3 limati: ‘Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.’ Kodi tingawathandize bwanji ophunzira Baibulo kukhala ndi chikondi pa Yehova? Pamene mukuphunzira, pezani mpata woti muziwathandiza kuyamikira kwambiri makhalidwe a Yehova. Muzinena mawu osonyeza kuti mumayamikira Mulungu kwambiri. Thandizani wophunzira kuti aziganizira zopanga ubwenzi wolimba ndi Yehova. Koposa zonse, kukonda Yehova kudzalimbikitsa ena ndiponso ifeyo kuti tizimvera Yehovayo kuchokera pansi pa mtima.—Mat. 22:37.

4. (a) Kodi n’chifukwa chiyani chitsanzo chathu chili chofunika? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi “mtima womvera”?

4 mwa Chitsanzo Chathu: Njira yabwino kwambiri yolimbikitsira ena kumvera uthenga wabwino ndiyo chitsanzo chathu. Komano, tifunikira kuchita khama nthawi zonse kuti tikhale ndi “mtima womvera.” (1 Maf. 3:9; Miy. 4:23) Kodi tingachite motani zimenezi? Dyetsani mtima wanu mwa kuchita phunziro lokhazikika la Baibulo ndi mwa kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse. (Sal. 1:1, 2; Aheb. 10:24, 25) Yanjanani ndi anthu amene mtima wawo umakonda kulambira koona. (Miy. 13:20) Muzipita mu utumiki wa kumunda nthawi zonse ndipo muzikhala ndi mtima wofuna kuthandiza anthu m’gawo lanulo. Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuumba mtima wanu kukhala wabwino. (Sal. 86:11) Pewani zinthu zimene zingawononge mtima wanu, monga zosangalatsa zolakwika ndi zachiwawa. Limbikirani kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuyandikira kwa Mulungu ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye.—Yak. 4:7, 8.

5 Kodi anthu omvera akudalitsidwa motani?

5 Yehova analonjeza anthu ake akale kuti adzawapatsa madalitso ochuluka akamvera mawu ake. (Deut. 28:1, 2) Chimodzimodzinso lerolino, Yehova akudalitsa kwambiri “iwo akumvera Iye.” (Mac. 5:32) Choncho, mwa kuphunzitsa ndi kupereka chitsanzo, tithandize ena kuti ayambe kumvera ndi mtima.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena