Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/05 tsamba 4
  • Zimene Utumiki Wathu Umakwaniritsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Utumiki Wathu Umakwaniritsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Pitirizani Kulalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Lalikani Uthenga Wabwino Mwachangu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupirira Muutumiki?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 11/05 tsamba 4

Zimene Utumiki Wathu Umakwaniritsa

1. Kodi Yehova amauona motani utumiki wathu, ndipo kodi anthu amaulandira bwanji uthenga wabwino?

1 Mawu a Mulungu amafotokoza kuti Akristu akuguba mosangalala mu utumiki wa Yehova, ngati kuti ali pachionetsero cha kupambana. (2 Akor. 2:14-16) Tikamadziwitsa anthu za Mulungu, utumiki wathu umakhala ngati zofukiza zonunkhira kwa Yehova. Anthu ena amakopeka ndi kukoma kwa uthenga wabwino, pomwe anthu ena amakana kumvetsera. Komabe kusamvetsera uthenga wabwino kwa anthu ambiri sikutanthauza kuti tikulephera ntchito yathu ayi. Tiyeni tione zimene utumiki wathu umakwaniritsa.

2. Kodi utumiki wathu umatithandiza kusonyeza chiyani?

2 Kulemekeza Yehova: Satana amanena kuti anthu amatumikira Yehova ndi zolinga za dyera. (Yobu 1:9-11) Utumiki wachikristu umatipatsa mwayi wosonyeza kuti kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndi koona. Ofalitsa ambiri amapitirizabe kumvera lamulo lolalikira ndi kupanga ophunzira ngakhale kuti ali ndi mavuto awo kapena anthu omwe amawalalikira alibe chidwi. Kupirira mokhulupirika koteroko kumakondweretsa mtima wa Yehova!—Miy. 27:11.

3. Kodi n’chifukwa chiyani tikufunikira kupitirizabe kudziwitsa anthu za dzina la Mulungu ndi cholinga chake?

3 Chinanso, utumiki wathu umathandiza kukwaniritsa zolinga za Mulungu. Pankhani yokhudza chiwonongeko cha dziko la Satanali chomwe chikubwera, Yehova amati: “Amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.” (Ezek. 39:7) Choncho kuti amitundu adziwe zimenezi, m’pofunika kwambiri kuti atumiki a Mulungu apitirizebe kulengeza za dzina la Yehova ndi cholinga chake kwa “mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.”—Chiv. 14:6, 7.

4. Kodi ntchito yolalikira imakhala bwanji maziko a chiweruzo?

4 Maziko a Chiweruzo: Kulalikira uthenga wabwino kulinso maziko a chiweruzo. Mtumwi Paulo anati Kristu Yesu adzabwezera chilango kwa “iwo osam’dziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Ates. 1:8, 9) Choncho anthu adzaweruzidwa mogwirizana ndi mmene angalandirire uthenga wabwino. Zimenezi zimapatsa atumiki a Mulungu udindo waukulu kwambiri! Pofuna kupewa mlandu wa magazi, sitiyenera kuleka kudziwitsa anthu za uthenga wa Ufumu wopulumutsa moyo umenewu.—Mac. 20:26, 27.

5. Kodi utumiki wathu umasonyeza bwanji chifundo cha Mulungu?

5 Tikamapitiriza kuthandiza anansi athu mwakhama kuti ayanjidwe ndi Mulungu, timaonetsa chifundo cha Yehova. (1 Tim. 2:3, 4) Podziwa kuti moyo wa anthu umasinthasintha, timawafikira anthuwo mobwerezabwereza ndi kuwalangiza kuti afunefune Yehova nthawi idakalipo. Potero, timasonyeza “mtima wachifundo wa Mulungu wathu,” amene ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’—Luka 1:78; 2 Pet. 3:9.

6. Kodi tingapindule bwanji pokhala otanganidwa ndi utumiki wa Yehova?

6 Kupindula Ife Eni: Kukhala otanganidwa ndi utumiki wa Yehova kumatiteteza. Kumatithandiza kukhala ‘oyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu’ ndiponso kupewa kuchitidwa mawanga ndi dongosolo la zinthu loipali. (2 Pet. 3:11-14; Tito 2:11, 12) Tiyeni tsopano tikhale “okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse,” podziwa kuti khama lathu pa utumiki wachikristu lipindula.—1 Akor. 15:58.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena