Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Ndilo Tiziphunzitsira Anthu
1 Tinasangalala kwambiri kuona buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? akulitulutsa pa Msonkhano Wachigawo wa “Kumvera Mulungu.” Anthu amene anabwera kumsonkhanowu anasangalala kwambiri kulandira buku lawolawo latsopanoli pa mapeto a pulogalamu, Loweruka. Kodi buku lophunzitsira latsopanoli lizigwiritsidwa ntchito motani? Analikonza kuti likhale buku limene tiziligwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu Baibulo. Ngakhale kuti buku latsopanoli tidzayamba ndi kuligwiritsa ntchito monga buku logawira m’mwezi wa March, tikulimbikitsa ofalitsa kuti ayambe panopo kugwiritsa ntchito bukuli poyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo.
2 Maphunziro a Baibulo Amene Mukuchititsa Panopa: Ofalitsa amene akuchititsa maphunziro a Baibulo ndi buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Amafunanji ayenera kuganizira kaye bwinobwino ngati kuli koyenera kuyamba kugwiritsa ntchito buku latsopanoli pa maphunziro awo ndiponso kuti angayambe liti. Ngati phunziro linalake lili la posachedwapa, mungathe kungoyambira kumayambiriro kwa buku latsopanoli. Ngati mwapita kale patsogolo mu buku la Chidziŵitso, mungathe kupitiriza phunzirolo mu chaputala chofanana nacho cha m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati mwatsala pang’ono kumaliza buku la Chidziŵitso, mwina ndi bwino kungomaliza bukulo.
3 N’zosakayikitsa kuti tonsefe tikudziwa anthu ambiri amene angapindule pophunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mukamayambitsa phunziro la Baibulo ndi munthu aliyense yesetsani kugwiritsira ntchito buku lophunzitsa mwatsatanetsataneli. Mwachitsanzo, anthu amene anaphunzirapo bulosha la Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso koma sanafike podzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa angafune kupitiriza maphunziro awo pogwiritsira ntchito buku latsopanoli. Makolo angasankhe kugwiritsira ntchito bukuli akamaphunzitsa ana awo mfundo zoona zokhudza chifuniro cha Mulungu.—Akol. 1:9, 10.
4 Kuphunzira Buku Lachiwiri: Kodi pali dongosolo lililonse loti wophunzira Baibulo aziphunzira buku lachiwiri akamaliza buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Inde. Ngati zikuoneka kuti wophunzira akupita patsogolo, ngakhale mwapang’onopang’ono, ndiponso kuti wayamba kuyamikira zimene akuphunzira, mungathe kupitiriza phunziro la Baibulolo pogwiritsira ntchito buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. Sitikukayika n’komwe kuti buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani litithandiza kwambiri pa ntchito yathu yopanga ophunzira.—Mat. 28:19, 20.