Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Okoma Mtima ndi Oganizira Ena
1 Ngakhale kuti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, iye ndi wokoma mtima, woganizira ena ndi waulemu. Amasonyeza makhalidwe amenewa akamachita zinthu ndi anthu opanda ungwiro. (Gen. 19:18-21, 29) Tingathe kukometsera uthenga wabwino umene timalalikira potsanzira Mulungu wathu wachisomo. (Akol. 4:6) Kuchita zimenezi kumafuna zambiri koposa kungolankhula molemekeza ena ndi mowapatsa ulemu.
2 Polalikira Khomo ndi Khomo: Bwanji ngati titapeza munthu panyumba panthawi yolakwika kapena ali wotanganidwa kwambiri moti sangathe kulankhula nafe? Ndi bwino kuzindikira kuti tam’dodometsa munthuyo ndipo tingafunikire kukambirana naye mwachidule kapena kum’pempha kuti tibwerenso nthawi ina. Ngati tili okoma mtima, sitingakakamize anthu kulandira mabuku kapena magazini athu pamene iwo sakufuna. Kuganizira ena kungatichititsenso kuti tizilemekeza katundu wawo, zimene zingafune kuti tizitseka zitseko za nyumba ndi za mipanda yawo ngati kungakhale koyenera kutero ndi kuphunzitsa ana athu kuchita zomwezo. Tiyeneranso kuonetsetsa kuti magazini kapena mabuku amene tasiya pakhomo popanda anthu, sakuonekera poyera. Ndithudi, kukoma mtima kungatipangitse kuti tiziwachitira ena zinthu zabwino zonga zomwe tingafune kuti iwonso atichitire.—Luka 6:31.
3 Polalikira Mumsewu: Polalikira mumsewu tingasonyeze kuti timaganizira ena ngati sitikutchingira ena njira kapena ngati sitikuunjikana kutsogolo kwa malonda a anthu ena. Tifunikiranso kuzindikira mwachangu zofuna za ena, kuonetsetsa kuti tikulankhula ndi anthu okhawo amene ali ndi nthawi kusiyana ndi kuumiriza anthu amene akufulumira. Nthawi zina tingafunikire kulankhula mokweza ndithu kuti ena atimve, makamaka pamene kuli phokoso. Komabe, tifunikira kuchita zimenezi mwaulemu, osati modzionetsera ayi.—Mat. 12:19.
4 Polalikira Patelefoni: Kuganizira ena kungatichititse kuti tiziimba foni pamalo opanda phokoso pochita ulaliki wa patelefoni. Munthu wakhalidwe labwino amayamba n’kuzidziwikitsa yekha kaye, ndiyeno n’kufotokoza cholinga chimene waimbira telefoni. Kulankhula mwaubwenzi ndiponso kulunjikitsa bwino mawu mu foni kumachititsa munthu amene mukulankhula nayeyo kumasuka kukambirana nanu nkhani ya m’Malemba. (1 Akor. 14:8, 9) Mwa kukhala anthu okoma mtima, oganizira ena, ndi aulemu m’njira zosiyanasiyana zimenezi, timakhala tikutsanzira Mulungu wathu wokoma mtima, Yehova.