Thandizani Ophunzira Baibulo Kuyamikira Makhalidwe Osayerekezereka a Yehova
1 Tikakhala mu utumiki, timachita zambiri osati kungowaphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo basi. Timathandiza anthu kum’dziwa Yehova monga weniweni ndi kuyamikira makhalidwe ake osayerekezereka. Anthu oona mtima akaphunzira choonadi chonena za Mulungu, amakhudzidwa mtima kwambiri, ndipo amalimbikitsidwa kusintha moyo wawo ‘kuti ayende koyenera Ambuye kum’kondweretsa monsemo.’—Akol. 1:9, 10; 3:9, 10.
2 Buku Latsopano Lophunzitsira: M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, makhalidwe a Yehova akutchulidwa kuyambira kumayambiriro kwenikweni. Mutu woyambirira weniweniwo, ukuyankha mafunso akuti: Kodi Mulungu amakuganiziranidi?, Kodi Mulungu ndi wotani?, ndiponso Kodi n’zotheka kumuyandikira Mulungu? Mutu woyamba womwewu ukufotokozanso kuti Yehova ndi woyera (ndime 10), wachilungamo ndi wokoma mtima (ndime 11), komanso wachikondi (ndime 13), wamphamvu (ndime 16), wachifundo ndi wachisomo, wokhululuka msanga, woleza mtima, ndi wokhulupirika (ndime 19). Pofotokoza nkhaniyi mwachidule, ndime 20 ikuti: “Mukamaphunzira zambiri za Yehova, m’pamenenso amakhala weniweni kwambiri kwa inu, ndipo mumafika pom’konda kwambiri ndi kumuyandikira.”
3 Kodi tingaligwiritse ntchito motani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuthandizira ophunzira Baibulo kukhala paubwenzi ndi Yehova? Pambuyo pokambirana ndime yonena za khalidwe lina la Mulungu, tingafunse wophunzira wathu kuti, “Kodi zimenezi zikukuuzani chiyani ponena za Yehova?” kapena “Kodi zimenezi zikusonyeza motani kuti Mulungu amasangalala nanu?” Mwa kugwiritsa ntchito mafunso amenewa pa phunziro, wophunzira wanu amaphunzira kusinkhasinkha pa zimene akuphunzira ndipo zimam’thandiza kukulitsa kuyamikira kwake makhalidwe osayerekezereka a Yehova.
4 Gwiritsani Ntchito Bokosi la Kubwereza: Mukamaliza kuphunzira mutu uliwonse, pemphani wophunzirayo kuti afotokoze m’mawu akeake mfundo zonse za m’bokosi lakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa.” Kambiranani malemba oikidwa pamapeto pa mfundo iliyonse. Polimbikitsa wophunzira kunena zimene zili m’mtima mwake, nthawi zina mungam’funse kuti, “Kodi mukuziona bwanji zimene Baibulo limaphunzitsa pa mfundo imeneyi?” Potero, sikuti mumangom’thandiza kumvetsa mfundo zazikulu za mutu umenewo koma mumazindikiranso bwino zimene wophunzira wanu amakhulupirira. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti wophunzira ayambe kukhala paubwenzi ndi Yehova.