Magazini Yapadera ya Galamukani! Yodzagawira mu September
1 Pafupifupi aliyense amasangalala kumva kulira kwa mbalame kapena kuona zimene zimachitika dzuwa likamalowa. Komabe, ambiri savomereza kuti Atate wakumwamba wachikondi ndiye analenga zinthu zimenezi. Posachedwapa, tikhala ndi mwayi waukulu kwambiri wouza anthu kuti Yehova ndiye Mlengi, pogawira magazini yapadera ya Galamukani! (Yes. 40:28; 43:10) Magazini yonse ya Galamukani! ya mwezi wa September idzakhala ndi nkhani zofotokoza mutu wakuti “Kodi Kunja Kuno Kuli Mlengi?”
2 M’gawo Lathu: Ngati mungathe, konzani zodzachita nawo ulaliki wa kukhomo ndi khomo pamodzi ndi mpingo wanu Loweruka lililonse. Dzakhaleni omasuka kugawira magazini yapaderayi nthawi zinanso m’kati mwa mlungu. N’zosakayikitsa kuti aphunzitsi ndi anthu enanso ambiri ogwira ntchito za maphunziro adzaikonda kwambiri magazini imeneyi. Motero mungadzakonze dongosolo lapadera kuti mupite kwa anthu amenewa omwe angakhale m’gawo lanu.
3 Ngati munthu wasonyeza chidwi, musiyireni funso loti mudzayankhe paulendo wotsatira. Mwachitsanzo, mungafunse funso lofuna kudziwa chifukwa chimene Mlengi wachikondi angalolere kuti anthu azivutika. Ndiyeno, paulendo wobwereza, mungam’sonyeze munthuyo mutu woyamba kapena mutu 11 wa m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kapena mungakonde kufunsa funso lokhudza cholinga chimene Mlengi ali nacho cha dziko lapansili, n’kudzakambirana naye mutu 3 paulendo wobwereza.
4 Kusukulu: Ngati muli pasukulu, bwanji osagawira Galamukani! yapadera imeneyi monga mphatso kwa aphunzitsi anu ndi kwa ana a sukulu anzanu? Kungokhala ndi magazini amenewa padesiki panu, kungachititse kuti ena afunse mafunso okhudza zimene timakhulupirira. Sitikukayikira kuti magazini imeneyi idzakuthandizani kufotokoza chikhulupiriro chanu mukamakambirana m’kalasi kapena polemba chimangirizo. Pokuthandizani kuchita zimenezi, mbali ya magaziniyi yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” ili ndi mutu wakuti “Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Chilengedwe?”
5 Yehova ndi woyenerera kulandira ulemerero ndi ulemu chifukwa cha zomwe analenga. (Chiv. 4:11) Tingapereke ulemu kwa Mlengi wathu ndi kuthandizanso ena kuchita zomwezi, mwa kugawira ndi mtima wonse magazini ya Galamukani! ya mwezi wa September.