Thandizani Ena Kukhala Mabwenzi a Mulungu
1 Masiku ano, anthu a mitundu yonse akuphunzitsidwa njira za Yehova. (Yes. 2:2, 3) Komano, kuti anthu amenewa ‘abereke zipatso mwa kupirira,’ ayenera kukonda Yehova. (Luka 8:15; Marko 12:30) Popanda chikondi chotero, sangakhale ndi mphamvu zopewera zoipa kapena zochitira zinthu zabwino. Njira imodzi yothandizira ena kuti akhale paubwenzi wabwino ndi Yehova ndiyo kuwathandiza kuti aziyamikira kwambiri makhalidwe ake. Alimbikitseni kuti aganizire mwakuya mfundo zimene zili m’buku la Yandikirani kwa Yehova.
2 Chitsanzo Chanu: Mmene mumachitira zinthu pamoyo wanu zingakhudze kwambiri mtima wa ophunzira Baibulo. Akaona kuti inuyo mumaona ubwenzi wanu ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali ndiponso mmene umakhudzira moyo wanu, nawonso angafune kuti akhale paubwenzi woterowo ndi Yehova. (Luka 6:40) Zoona zake n’zakuti anthu nthawi zambiri amatsatira zochita zathu osati zonena zathu.
3 Njira yaikulu imene makolo amaphunzitsira ana awo kukonda Yehova ndiyo kuwasonyeza chitsanzo chabwino. (Deut. 6:4-9) Banja lina lomwe linkafuna kulera ana awo m’choonadi linafunsira malangizo kwa makolo ena amene anakwanitsa kuchita zimenezi. “Mfundo imodzi yofanana imene ndinauzidwa ndi aliyense amene ndinalankhula naye, ndi yoti chinthu chofunika kwambiri ndi chitsanzo chabwino cha makolo,” anatero mwamunayo. Choncho, mmene makolo amachitira pa moyo wawo angapereke chitsanzo chabwino kwa ana awo cha zimene kukhala “bwenzi la Mulungu” kumatanthauza.—Yak. 2:23.
4 Mapemphero Ochokera Pansi pa Mtima: Mungathandizenso ena kuti akhale paubwenzi ndi Yehova mwa kuwaphunzitsa kuti azipemphera kuchokera pansi pa mtima. Mungawasonyeze pemphero la Yesu la chitsanzo ndiponso mapemphero ena ambiri ochokera mumtima amene ali m’Malemba. (Mat. 6:9, 10) Mungaphunzitse ana anu komanso ophunzira Baibulo anu kupemphera akamamvetsera mmene inuyo mumapempherera. Iwo akamamva mawu anu ochokera pansi pa mtima, angadziwe mmene inuyo mumamuonera Yehova. Alimbikitseni kuti ‘alimbikirebe m’kupemphera’ akamakumana ndi ziyeso. (Aroma 12:12) Akamalandira thandizo la Yehova m’nthawi zovuta, angayambe kum’khulupirira ndi kum’konda monga bwenzi lawo lenileni.—Sal. 34:8; Afil. 4:6, 7.