Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec.15
“Panthawi ino ya pachaka, anthu ambiri amaganizira mawu amene angelo analengeza pa kubadwa kwa Yesu. [Werengani Luka 2:14.] Kodi mukuganiza kuti mtendere udzabweradi padziko lapansi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza momwe Yesu adzabweretsere mtendere weniweni posachedwapa padziko lapansi.”
Galamukani! Dec.
“Anthu achipembedzo ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kumwa mowa. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amakuona bwanji kumwa mowa? [Yembekezani ayankhe.] Ngakhale kuti chozizwitsa choyamba cha Yesu chinali kusintha madzi kukhala vinyo, Baibulo limaperekanso chenjezo ili. [Werengani Miyambo 20:1.] Nkhani iyi ikufotokoza maganizo abwino a m’Baibulo pankhani imeneyi.” Sonyezani nkhani imene yayambira pa tsamba 18.
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Kodi mukuganiza kuti kuchuluka kwa chuma chimene munthu ali nacho n’kumene kumasonyeza kuti zinthu zikumuyendera bwino kapena ayi? [Yembekezani ayankhe. Kenaka werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.] Ngakhale kuti Baibulo silidana ndi ndalama, limasonyeza kuti, kuti munthu zinthu zimuyenderedi bwino sizidalira chuma. Magazini iyi ikufotokoza zimenezo.”
Galamukani! Jan.
“Kodi mukuganiza kuti tidzaona izi zikuchitika? [Werengani Yesaya 33:24. Kenaka yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene sayansi ya zamankhwala yakwanitsa kuchita ndi mmene lonjezo la m’Baibulo lidzakwaniritsidwire.”