Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 6
  • Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kodi Mwakonzekera Ngati Mutachita Ngozi?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 6

Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?

1 Kodi dokotola wina ananena chiyani pankhani ya chithandizo chopanda magazi?

1 “Odwala aliyense amene amathandizidwa popanda magazi ndiye kuti akulandira chithandizo chapamwamba kwambiri.” Anatero Dr. Michael Rose, mkulu wa pachipatala chinachake, yemwenso ndi dokotola wogonetsa anthu powachita opaleshoni.

2. Pofuna chithandizo cha mankhwala, kodi Akhristu oona amaganizira chiyani?

2 Anthu ambiri amalola kuthandizidwa m’njira iliyonse imene ikuoneka kuti iwachiritsa mwamsanga, ngakhale njira yodziwika kuti imabweretsa mavuto ena a thanzi, monga chithandizo choika munthu magazi. Koma Mkhristu weniweni amayesetsa kuona nkhaniyi mwakuya, komanso mosamala ndipo saona kuti chinthu chachikulu kwa iye ndi kuchira kokhako basi. Mboni za Yehova zimayamikira ntchito yoyesetsa kupereka chithandizo chabwino kwambiri chamankhwala, ndipo zimaonetsetsa kuopsa ndi ubwino wa chithandizocho. Komabe, pa za chithandizo chokhudza zinthu zochokera ku magazi, Mboni za Yehova zimaganizira bwinobwino zimene Mulungu amanena ndipo zimaganiziranso ubwenzi wawo ndi Wopatsa Moyoyu.—Sal. 36:9.

3. Kodi chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimakanira kuikidwa magazi n’chiyani?

3 Ngakhale kuti kukana kulandira magazi kumatipindulitsa m’njira zambiri zokhudza thanzi lathu, timakana kutero pa zifukwa zokhudza kupembedza. Choncho, chifukwa chachikulu chokanira kulandira magazi n’chakuti timafuna kumvera lamulo la m’Baibulo lakuti tisale mwazi.—Mac. 15:28, 29.

4. Kodi madokotala ndi manesi ena amachita chiyani?

4 Koma ngakhale kuti pali umboni wochuluka zedi wakuti chithandizo chopanda magazi n’chabwino, madokotala ndi manesi ena amalimbanabe n’kunyengerera kapena kuopseza a Mboni ena amene akudwala kuti avomere kuikidwa magazi.

5. Kodi malamulo a dziko lino amati chiyani pa za ufulu umene munthu ali nawo?

5 Buku la Malamulo Oyendetsera Dziko la Malawi, mu Chaputala 4, Gawo 33, limati munthu ali ndi ufulu wa chikumbumtima, wa chipembedzo, ndi wa chikhulupiriro.

6. Kodi n’chiyani chimene tingachite ngati dokotala wakakamiza wodwala kuikidwa magazi koma wodwalayo atanena bwinobwino kuti sakufuna?

6 Motero, Mkhristu ali ndi ufulu wodula chisamani ngati dokotala kapena chipatala chitaphwanya lamulo la dziko lino pokakamiza odwala kulandira chithandizo chimene sakufuna. Mkhristuyo angapemphe thandizo kwa akulu a mumpingo wake, Komiti Yolankhulana ndi Achipatala ya kwawoko ndiponso ofesi ya nthambi ngati angafunikire thandizo lotere. N’zodziwikiratu kuti milandu ngati imeneyi munthu sangaluze, motero imathandiza kuti madokotala okonda kuthandiza odwala m’njira zosavomerezeka aziopa kutero.—Afil. 1:7.

7. Kodi Akhristu onse ali ndi udindo wotani, ndipo angaukwaritse motani?

7 Komabe, ndi udindo wathu patokhapatokha komanso monga banja kusamalira thanzi lathu. N’chinthu chanzeru kuthamangira kuchipatala ndi anthu a m’banja mwathu amene akudwala, makamaka ana ndiponso amayi oyembekezera, tikangoona kuti anthuwo akudwala, kuopera kuti zinthu zingachite kufika poipa. Ana, amayi oyembekezera ndiponso achikulire ayenera kudya zakudya za magulu atatu. Zakudya zambiri za magulu atatu zimapezeka kwathu kuno, monga masamba, zipatso, phala la soya, phala la mgaiwa lothira nsinjiro, futali, mbatata, nyemba, mazira, ndi zakudya zina. Kawirikawiri anthu athanzi sadwala matenda ochepa magazi m’thupi.

8. (a) Kodi tingathandize bwanji madokotala ofuna kutithandiza? (b) Kodi Yehova amachita motani zinthu ndi anthu ake okhulupirika?

8 Madokotala siziwavuta kupereka chithandizo chamankhwala chapamwamba (chomwe n’chithandizo chopanda magazi) kwa anthu amene amadzisamalira bwino kwambiri ndiponso kwa anthu amene ali ndi njira zabwino zopezera chithandizo cha mankhwala. N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti Yehova amadalitsa anthu ake okhulupirika m’mbali zonse za moyo wawo, ngakhalenso mbali yofuna chithandizo chabwino chamankhwala.—Sal. 97:10.

9. Kodi achibale anu omwe si Mboni ayenera kudziwa chiyani pa zimene mwasankha zokhudza chithandizo chamankhwala?

9 Kodi mwasankha njira zolowa m’malo mwa magazi ziti zimene mukufuna kugwiritsa ntchito inu ndi ana anu? Achibale anu omwe si Mboni ayeneranso kudziwitsidwa bwino za zosankha zanu ndiponso zifukwa zimene mwasankhira zimenezo.—Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, ndi ya October 15, 2000.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena