Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June 15
“Kodi mwaona kuti anthu ambiri masiku ano akutsatira mfundo zawozawo pankhani ya makhalidwe abwino kapena oipa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chitsanzo cha malangizo odalirika opezeka m’Baibulo. [Werengani limodzi la malemba omwe ali m’bokosi pamasamba 6 ndi 7.] Magaziniyi ikufotokoza mmene timapindulira tikamatsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene zili m’Baibulo.”
Galamukani! June
“Tonsefe timafunikira ndalama kuti tipeze zofunika pamoyo. Koma kodi mukuganiza kuti ndi bwino kuti munthu azikonda kwambiri ndalama? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene lembali likunena pa nkhani yokonda ndalama. [Werengani 1 Timoteyo 6:10.] Magaziniyi ili ndi mfundo zothandiza za mmene munthu angakhalire ndi moyo wosalira zambiri.”
Nsanja ya Olonda July 1
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani anthu ena amavutitsidwa chifukwa chosiyana mtundu, mayiko, kapena chinenero? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chimene chili pa lembali. [Werengani 1 Yohane 4:20.] Magaziniyi ikuyankha funso lakuti, Kodi anthu osiyana mitundu angagwirizane?”
Galamukani! July
“Mosiyana ndi nyama zimene zimangochita zinthu mosaganiza, anthu amatha kusankha mfundo zoti ayendere pa moyo wawo. Kodi mukuganiza ndi kuti kumene tingapeze malangizo odalirika? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Sal. 119:105.] Magaziniyi ikufotokoza mmene malangizo a m’Baibulo alili othandiza kwambiri.”