Tiziyesetsa Kuwonjezera Utumiki Wathu
1 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuyenda m’njira ya Mulungu ndi ‘kupitiriza kutero mowonjezereka.’ (1 Ates. 4:1) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tizichita chiyani? Chinthu chimodzi chimene tiyenera kuchita n’choti tiziyesetsa nthawi zonse kupeza njira za mmene tingawonjezerere zinthu zauzimu zimene timachita, ndipo tiyenera kuyesetsa ‘kukwaniritsa utumiki wathu bwino lomwe.’—2 Tim. 4:5.
2 Chifukwa Chowonjezerera Utumiki: Timayesetsa kuwonjezera zimene timachita mu utumiki wathu chifukwa timafunitsitsa kutumikira Mlengi wathu mokwanira. Timafuna kukula mwauzimu ndiponso timafuna kuchita bwino kwambiri muutumiki. Kukhala ndi ndandanda yabwino ndiponso kuchita utumiki pachifukwa chabwino kungatithandize kukwaniritsa zolinga zathu zauzimu.—Sal. 1:1, 2; Afil. 4:6; Aheb. 10:24, 25.
3 Kuti tithe kuwonjezera zimene timachita mu utumiki, timafunikira kukhala ndi mtima wopatsa ndiponso wodzipereka. Kupemphera ndi kusinkhasinkha za chitsanzo chabwino cha Yesu kungatithandize kukhala ndi mtima umenewu. (Mat. 20:28) Pochita utumiki wake, Yesu anali wosangalala kwambiri chifukwa chotumikira anthu ena. (Mac. 20:35) Tingatsanzire Yesu mwa kusonyeza kwambiri anthu chidwi ndiponso mwa kukhala tcheru kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tiwonjezere utumiki wathu.—Yes. 6:8.
4 Zimene Makolo Angachite: Tingathandize ana aang’ono kuti ayambe kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri muutumiki. Ana amaona khama limene anthu a m’banja mwawo ali nalo ndiponso zimene iwowo akuchita kuti awonjezere utumiki wawo. Ali mnyamata, mbale wina analimbikitsidwa kuchita zambiri muutumiki chifukwa chochita zinthu zauzimu limodzi ndi agogo ake. Kuona khama ndi chimwemwe cha agogo akewo kunam’limbikitsa kuti azipeza mipata yotumikira abale ake. Tsopano mbaleyu ndi mtumiki wothandiza.
5 Abale Akufunika: “Ngati munthu aliyense akukalamira . . . , akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Mawu amenewa amalimbikitsa abale kukalamira kuti ayenerere udindo wowonjezereka m’gulu la Yehova. Iwo sayenera kukhala ndi luso kapena nzeru zapadera kuti achite zimenezi. Mbale amene akukalamira udindo amafuna Ufumu choyamba ndipo amachita changu muutumiki. (Mat. 6:33; 2 Tim. 4:5) Amayesetsanso kukhala chitsanzo chabwino kwa anthu ena.
6 Padziko Lonse: Yehova akufulumiza ntchito yosonkhanitsa anthu. (Yes. 60:22) Choncho n’kofunika kwambiri kuti anthu onse amene akutsatira chitsanzo cha Yesu awonjezere zimene amachita mu utumiki. Lipoti lapadziko lonse la chaka chautumiki cha 2006 linati, anthu okwanira 248,327 anabatizidwa m’chakachi. Chiwerengero chimenechi chikusonyeza kuti paavereji anthu 680 ankabatizidwa tsiku lililonse. Choncho tiyeni tonsefe tiyesetse kupeza njira zowonjezerera utumiki wathu.