Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/08 tsamba 6
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Tisawaiwale Ngakhale Amakhala Kwaokha
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kusamalira Okalamba—Vuto Lomakulakulabe
    Galamukani!—1991
  • Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Ntchito Yofunika ya Anamwino
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 4/08 tsamba 6

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi n’koyenera kuti Mkhristu wa Mboni za Yehova apite ku chipatala choyendetsedwa ndi bungwe lachipembedzo?

Mabungwe ambiri achipembedzo ali ndi zipatala kapena nyumba zosamalira odwala omwe ali ndi matenda otenga nthawi yaitali. Nthawi zambiri, mabungwewa satsegula zipatala ndi nyumba zimenezi n’cholinga chopititsa patsogolo zimene Babulo Wamkulu amaphunzitsa. (Chiv. 18:2, 4) Mwina cholinga chake choyambirira chinali kupezera ndalama bungwe lachipembedzolo. Masiku ano zipatala zina zili ndi mayina achipembedzo chifukwa chakuti zinatsegulidwa ndi bungwe lachipembedzo, pamene zina zili ndi antchito ambiri omwe ndi atsogoleri achipembedzo.

Ngati Mkhristu wa Mboni za Yehova akufuna kupita ku chipatala kapena kunyumba yosamalira odwala, zili kwa iye kusankha kupita ku chipatala kapena kunyumba yomwe n’kutheka kuti imayendetsedwa ndi bungwe lachipembedzo. Chikumbumtima cha Mkhristu wina chingamulole kuchita zimenezi, pamene wina sichingamulole. (1 Tim. 1:5) Pali zinthu zingapo zimene zingakhudze zosankha za munthu pankhaniyi ndipo ndi bwino kuti tione zinthu zimenezi.

Mwachitsanzo, zingatheke kuti chipatala kapena nyumba yosamalira odwala yomwe ili ndi dzina lachipembedzo ndi yokhayo imene ili pafupi. Kapena mwina pali chipatala china pafupi, koma chipatala chomwe chikuyendetsedwa ndi achipembedzo n’chimene chimathandiza bwino kwambiri. Chipatala chomwe chili ndi dzina lachipembedzocho chingakhale kuti ndi chokhacho chimene chingathandize bwino pa matenda enaake, mwinanso chingakhale chipatala chokhacho chimene dokotala wanu amagwirako ntchito. Komanso nthawi zina zipatala zoyendetsedwa ndi bungwe lachipembedzo zingalemekeze maganizo anu pankhani ya magazi, pamene zipatala zina, ngakhalenso zaboma, sizingatero. Choncho, zimenezi ndi zina mwa zinthu zimene muyenera kuganizira mukamasankha chipatala chimene mukufuna kupitako.

Mukasankha kupita ku chipatala kapena kunyumba yosamalira odwala yomwe ikuyendetsedwa ndi bungwe lachipembedzo, mwina mungangolipira chithandizo chimene mwalandiracho. Chipatala kapena nyumbayo muzingoiona ngati bizinesi ya bungwelo ndipo ngati akuchitirani zinthu zinazake, inu n’kuwalipira, si ndiye kuti mukuthandiza chipembedzo chonyenga. Inuyo mukungolipira zinthuzo kapena ntchito imene akuchitiraniyo.

N’zoona kuti inuyo monga Mkhristu, zinthu zikafika pamenepa muyenera kuonetsetsa kuti musachite nawo chilichonse chokhudza kulambira konyenga. Komanso, anthu ogwira ntchito kumalowo kapena obwera kudzakuonani simungawatchule mayina achipembedzo amene iwo amagwiritsa ntchito, monga akuti “Abambo” kapena “Asisitere.” (Mat. 23:9) Muyenera kuonetsetsa kuti mwapita kumeneko kuti mukathandizidwe basi.

Pamene akukonza zokugonekani m’chipatala, mungawadziwitse kuti ndinu wa Mboni za Yehova ndiponso kuti mungasangalale kuchezeredwa ndi akulu a m’deralo. Izi zingathandize kuti mulandire chithandizo chauzimu choyenerera panthawi yomwe muli m’chipatalamo.—1 Ates. 5:14.

Achibale amene ndi Mboni, akulu ndi ena onse mumpingo, ayenera kusamalira zosowa zauzimu za m’bale kapena mlongo aliyense wachikulire wa mumpingo mwawo amene akukhala ku nyumba yosamalira odwala, makamaka imene ikuyendetsedwa ndi bungwe lachipembedzo. Tikachita zimenezi ndi mtima wonse, achikulire oterewa angalimbikitsidwe kwambiri ndiponso zingawathandize kuti asamachite nawo mapemphero, zikondwerero kapena zochitika zina za panyumbapo mosazindikira.

Malinga ndi mfundo zimene taonazi, aliyense payekha ayenera kuganizira mofatsa ndi kusankha chipatala kapena nyumba yosamalira odwala imene angapiteko.—Agal. 6:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena