Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda May 1
“Anthu ena akamaona kuchuluka kwa masoka achilengedwe, amaganiza kuti Mulungu akutilanga. Kodi maganizo anu ndi otani? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani 1 Yohane 4:8.] Nkhani iyi ikufotokoza chifukwa chake sitiyenera kumuimba mlandu Mulungu chifukwa cha mavuto obwera ndi masoka achilengedwe.” Asonyezeni nkhani imene ili pa tsamba 30.
Galamukani! May
Werengani Mateyo 6:10. Kenako funsani kuti: “Kodi mukudziwa kuti chifuniro cha Mulungu cha dziko lapansi n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena kuti Mulungu pachiyambi anali nalo cholinga dziko lapansili, ndipo cholingacho sichinasinthe. Nkhani iyi ikufotokoza zimenezi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 10.
Nsanja ya Olonda June 1
“Imodzi mwa nkhani zodziwika bwino m’Baibulo ndi nkhani ya Nowa ndi Chigumula. Kodi mumakhulupirira kuti Chigumula chinachitikadi? [Yembekezani ayankhe.] Zimene Yesu ananena zimasonyeza kuti chinachitikadi. [Werengani Luka 17:26, 27.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kuti Chigumula chinachitikadi ndiponso zimene tikuphunzirapo.”
Galamukani! June
“Kulera mwana ndi kovuta, makamaka akafika zaka zaunyamata, pamene zambiri zimasintha. Kodi mukuganiza kuti makolo angapeze kuti malangizo odalirika? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Yesaya 48:17, 18.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza makolo kulera ana awo mwanzeru.”