Kukonzekera ndi Chinsinsi cha Maulendo Obwereza Aphindu
1. Kodi utumiki wachikhristu m’nthawi ya Yesu unafunika kufutukulidwa motani?
1 Yesu anakonzekeretsa bwinobwino ophunzira ake kuti akhale alaliki ogwira mtima a “uthenga wabwino wa ufumu.” (Mat. 4:23; 9:35) Maphunzirowa anachitikira ku Palestina. Koma asanakwere kumwamba, Yesu anasonyeza kuti utumiki wachikhristu udzafutukulidwa kwambiri n’cholinga ‘chopanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.’—Mat. 28:19, 20.
2. Kodi kumvera lamulo la Yesu la ‘kupanga ophunzira’ kumaphatikizapo chiyani?
2 Ntchito imeneyo imaphatikizapo kubwerera kwa anthu amene achita chidwi ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene Khristu analamula. Kuti maulendo obwereza akhale aphindu, timafunika kukonzekera bwino.
3. Ngakhale paulendo woyamba, kodi mungatani kuti mutsegule njira ya ulendo wobwereza?
3 Konzekerani Pasadakhale: Ofalitsa ena amasiya funso akamaliza kukambirana ndi munthu pa ulendo woyamba ndipo amalonjeza kuti adzabweranso kuti adzakambirane yankho la funsolo. Iwo apeza kuti kugwiritsa ntchito mfundo za m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa ulendo wobwereza kwawathandiza kuyambitsa phunziro la Baibulo.
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchedwa ndi kudikira magazini atsopano kuti tipange ulendo wobwereza?
4 Popeza kuti timakhala ndi magazini amtundu umodzi mwezi wonse, sizikutanthauza kuti tiyenera kudikira magazini a mwezi wotsatira kuti tidzabwererenso kwa munthuyo. N’zotheka kukulitsa chidwi cha munthuyo mwa kukambirana naye mfundo za m’magazini imene ali nayo kale.
5. Kodi kukhala ndi cholinga kuli ndi phindu lanji?
5 Khalani ndi Cholinga: Musanabwerere kwa munthu, patulani mphindi zingapo kuona zimene munakambirana ndiponso cholinga cha ulendo wanu wobwerezawo. Mwachitsanzo, mungakambirane mfundo inayake m’buku limene munasiya. Kapena mungamusiyire buku lina logwirizana ndi zimene munakambirana ulendo woyamba. Ngati paulendo watha munasiya funso, ndiye kuti cholinga chanu chiyenera kuphatikizapo kukayankha funsolo. Pofuna kufotokoza lemba limene likutsindika mfundo imene mukunena, yesetsani kuwerenga lembalo m’Baibulo.
6. Kodi cholinga chathu n’chiyani popanga maulendo obwereza?
6 Cholinga Chathu: Musaiwale kuti cholinga chathu ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo. M’bale wina paulendo wobwereza anapempha mwininyumba kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo, koma munthuyo anakana. M’baleyu anabwereranso kwa munthuyu ndi magazini atsopano ndipo anati: “Ulendo uno, tikuyankha funso la m’Baibulo limene anthu amafunsa masiku ano.” Atamva maganizo a munthuyo, m’baleyu anawerenga lemba ndiponso ndime ina yogwirizana ndi lembalo m’buku logwiritsa ntchito pa phunziro la Baibulo. Mapeto ake, phunziro la Baibulo lokhazikika linayamba.
7. Kodi kukonzekera bwino kwakuthandizani bwanji kuyambitsa phunziro la Baibulo?
7 Kupatula nthawi yokonzekera maulendo obwereza kuli ndi phindu lake ngakhale kuti kumafuna khama. Chimwemwe chathu chimakula ndipo tingakhale ndi mwayi wothandiza munthu ‘amene ali ndi maganizo oyenerera’ kukhala pa njira ya kumoyo.—Mac. 13:48.