Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/09 tsamba 4-6
  • Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Misonkhano Yachigawo Ndi Nthawi Imene Timalambira Mulungu Mosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Masiku Atatu Otsitsimulidwa Mwauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Tsatirani Khristu Podzisungira Ulemu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 7/09 tsamba 4-6

Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?

1. Kodi pamafunika chiyani pokonzekera phwando?

1 Kuti phwando litheke pamafunika kukonzekera kwambiri. Pamafunika kugula zakudya ndiponso kuzikonza bwino. Pamafunikanso dongosolo labwino pogawa chakudyacho. Komanso pamafunika kukonza malo amene phwandolo lidzachitikire. Anthu oitanidwa ku phwandolo amafunika kukonzekera mmene adzayendere, makamaka ngati akuchokera kutali. Ngakhale kuti pamakhala ntchito yambiri yokonzekera phwando, zimasangalatsa kudya chakudya chokoma ndiponso chopatsa thanzi pamodzi ndi mabwenzi ndi achibale. Posachedwapa, ife Mboni za Yehova padziko lonse tidzasonkhana kuti tidzasangalale ndi phwando lauzimu lomwe takhala tikuliyembekezera kwanthawi yaitali. Phwando limeneli ndi Msonkhano Wachigawo wa mutu wakuti “Khalani Maso.” Ntchito yambiri yokonzekera msokhanowu yachitika kale. Tonse tikuitanidwa kumsonkhanowu. Kuti tikapezekepo ndiponso kuti tikapindule kwambiri ndi msonkhanowu, ifenso tifunika kukonzekera.—Miy. 21:5.

2. Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mudzapezeke pamsonkhanowu masiku onse?

2 Yesetsani Kuti Mudzapindule Kwambiri: Kodi mwakonza kale zodzapezeka pamsonkhanowu masiku onse? Ngati muli pantchito, pemphani abwana anu kuti adzakupatseni masiku a tchuthi n’cholinga choti mudzapezeke pamsonkhanowu kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza. Kodi mwakonza kale mmene mudzayendere ndiponso malo ogona? Akulu ayenera kuonetsetsa kuti okalamba, ofooka ndiponso ena amene akufunikira thandizo, asamalidwa.—Yer. 23:4; Agal. 6:10.

3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kupita kumsonkhano wa mayiko umene sitinaitanidwe?

3 M’madera ena mudzachitika misonkhano ya mayiko. Dziwani kuti amene ayenera kukapezeka pamisonkhano imeneyi ndi okhawo amene ali m’mipingo yoitanidwa komanso alendo oitanidwa ochokera m’mayiko ena. Pokonza misonkhano imeneyi, ofesi ya nthambi yaganizira kuchuluka kwa anthu oyenera kuwaitana, poona kukula kwa malo a msonkhano ndiponso malo ogona. Ngati ofalitsa angapite kumsonkhano wa mayiko umene sanaitanidwe, ndiye kuti anthu angadzapanikizane.

4. Kodi tifunikira kuchita chiyani tsiku lililonse msonkhano usanayambe?

4 Konzekerani kuti tsiku lililonse muzikafika pamalo a msonkhanowo nthawi yabwino kuti mukapeze malo okhala, msonkhano usanayambe. Kutatsala nthawi pang’ono kuti msonkhano uyambe, mungachite bwino kuoneratu pulogalamu. Zimenezi zingakuthandizeni kukonzekera bwino nkhani zimene zikambidwe. (Ezara 7:10) Tcheyamani wa msonkhano akalengeza kuti nyimbo zamalimba zikuyamba, mvetserani ndipo konzekerani kuimba nawo nyimbo yotsegulira misonkhano ndiponso kumvetsera pemphero.

5. Kodi tingatani kuti banja lathu lipindule kwambiri ndi msonkhano?

5 Ngati banja lonse litakhala pamodzi, makolo angathe kuonetsetsa kuti ana awo akumvetsera msonkhanowo mwachidwi. (Deut. 31:12) Aliyense akulimbikitsidwa kutsatira wokamba nkhani akamawerenga malemba m’Baibulo. Kulemba mfundo zachidule kungakuthandizeni kuti muzimvetsera mwachidwi. Ndipo mfundo zimene mwalembazo zidzakuthandizaninso kukumbukira mfundo zikuluzikulu za msonkhanowo. Pewani kulankhulana mwachisawawa komanso kuyendayenda msonkhano uli mkati. Ngati muli ndi foni ya m’manja, onetsetsani kuti isakusokonezeni kapena kusokoneza ena pamsonkhanopo. Tsiku lililonse msonkhano ukatha, mungachitenso bwino kukambirana ndi ena mfundo zimene zakusangalatsani pamsonkhanopo.

6. Kodi ndi mwayi wotani umene timakhala nawo pamisonkhano yathu, ndipo tingatani kuti tiugwiritse ntchito bwino?

6 Pamisonkhano yachigawo, timakhala ndi mwayi wocheza ndi abale ndiponso alongo athu ndipo mwayi umenewu sitingaupeze kwina kulikonse. (Sal. 133:1-3; Maliko 10:29, 30) Mungachite bwino kugwiritsa ntchito mwayi umenewu kuti mudziwane ndiponso mucheze ndi anthu amene mwayandikana nawo panthawi yopuma. N’chifukwa chake ndi bwino kutengeratu chakudya choti mukadyere kumsonkhano m’malo mopita kukadya ku lesitilanti. Muonetsetse kuti mwayi wolimbikitsana umenewu usakudutseni.—Aroma 1:11, 12.

7. Kodi tiyenera kuganizira chiyani pankhani ya zovala kumsonkhano?

7 Kavalidwe: Yehova analamula Aisiraeli kuti aziika mphonje ndiponso thonje la buluu mphepete mwa zovala zawo. (Num. 15:37-41) Zovalazi zinkawakumbutsa kuti iwo anali anthu amene Yehova anawapatula kuti azimulambira. Masiku anonso, timasiyana ndi dziko tikavala modzilemekeza pamsonkhano. Zimathandizanso kuti tilalikire mosavuta anthu amene timakumana nawo pamene tachoka pamalo a msonkhano, kupita kokadya ku lesitilanti madzulo. Choncho, muyenera kuganizira bwino zovala zimene mukufuna kudzavala.

8. Kodi tingatani kuti tidzalalikire m’dera limene mukuchitikira msonkhano?

8 Mudzayesetse Kulalikira: Ngati takonzekera, tingadzathe kulalikira anthu m’dera limene mudzachitikire msonkhano. M’bale wina atapita ku lesitilanti ndi mkazi wake msonkhano utatha, anangogwira baji yake ya msonkhano n’kufunsa woperekera zakudya kuti: “Kodi mwaona anthu ambiri atavala mabaji otere?” Woperekera zakudyayo anayankha kuti waona koma sakudziwa kuti mabajiwo ndi a chiyani. Zimenezi zinathandiza kuti ayambe kukambirana, moti m’baleyu anaitanira munthuyo kumsonkhanowo.

9. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira Yehova, yemwe watikonzera phwandoli?

9 Ngakhale kuti abale athu ndi amene adzakambe nkhani, kufunsa mafunso ndiponso kuchita zitsanzo, Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi amene amakonza phwando lauzimu la chaka ndi chaka limeneli. (Yes. 65:13, 14) Tingasonyeze kuyamikira amene watikonzera phwandoli, yemwe ndi Yehova, ngati tidzapezekepo masiku onse ndi kudya nawo chakudya chonse chauzimu chimene chidzaperekedwe. Kodi mwakonzekera kale kudzapezeka pamsonkhanowu?

[Bokosi patsamba 6]

Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo

◼ Nthawi ya Misonkhano: Masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba 8:20 m’mawa. Kutatsala mphindi zochepa kuti chigawo cha msonkhano chiyambe, tcheyamani azidzakhala papulatifomu, nyimbo za Ufumu zamalimba zili mkati. Nyimbo zamalimba zikayamba tonse tiyenera kukhala pansi kuti msonkhano uyambe mwadongosolo. Lachisanu ndi Loweruka msonkhano udzatha 3:55 madzulo, ndipo Lamlungu udzatha 3:00 madzulo.

◼ Koimika Galimoto: Malo onse ochitira msonkhano adzakhala ndi malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto afunikira kudzaonetsetsa kuti zitseko za magalimoto azitseka bwinobwino, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.

◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.

◼ Chakudya Chamasana: Tikulimbikitsidwa kuti tidzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochitika zapadera monga tchipisi, zipatso, mpunga wophika, mbatata, chinangwa, mtedza wokazinga ndi zakumwa. Koma osabweretsa mowa pamalo a msonkhano.

◼ Zopereka: Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu mwa kupereka mwaufulu ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Tingapereke ndalamazi ku Nyumba ya Ufumu yathu kapena pamsonkhanopo. Polemba macheke operekedwa pamsonkhano wachigawo, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku “Watch Tower.”

◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati munthu wadwala mwadzidzidzi pamsonkhanopo, dziwitsani akalinde amene ali pafupi. Iwo angadziwitse mwamsanga Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo aone mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.

◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’Chinenero cha Manja, ku msonkhano wachigawo wa Chingelezi wa ku Blantyre ndi ku Lilongwe. Zimenezi zidzalengezedwa patsiku loyamba la msonkhanowo m’chigawo choyamba.

◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira mawu ku magetsi kapena ku zokuzira mawu za pamsonkhano ndiponso muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisadzasokoneze ena.

◼ Mafomu Odziwitsira Ena za Munthu Wachidwi: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi panthawi ya msonkhano, gwiritsani ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa adzabweretse fomu imodzi kapena awiri kumsonkhanowu. Mungapereke mafomu olembedwa bwinobwino ku dipatimenti ya mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mutabwerako kumsonkhanowo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2005, tsa. 6.

◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli mkati.

◼ Mafoni a M’manja: Muyenera kuthimitsa kapena kuwatchera kuti asalire n’kusokoneza ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena