Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/09 tsamba 1
  • Timasonyeza Kuti Timakonda Mulungu mwa Utumiki Wathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timasonyeza Kuti Timakonda Mulungu mwa Utumiki Wathu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kondani Mulungu Amene Amakukondani
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Chikondi Ndi Khalidwe Lamtengo Wapatali Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kulani M’chikondi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Uzikonda Yehova Mulungu Wako”
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 6/09 tsamba 1

Timasonyeza Kuti Timakonda Mulungu mwa Utumiki Wathu

1. Kodi kukonda Mulungu kunam’pangitsa Yesu kuchita chiyani?

1 Chikondi chinam’pangitsa Yesu kuchita utumiki. Utumiki wonse wa Yesu ndi umboni wamphamvu wakuti amakonda Yehova. Yesu anati: “Kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atateyo anandipatsa.” (Yoh. 14:31) Monga otsatira mapazi a Yesu, ifenso tili ndi mwayi wosonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu mwa utumiki wathu.—Mat. 22:37; Aef. 5:1, 2.

2. Kodi kukonda Yehova kumakhudza bwanji utumiki wathu?

2 “Dzina Lanu Liyeretsedwe”: Tikakhala achangu pogwiritsa ntchito mpata uliwonse kuuza anthu za Yehova ndi Ufumu wake, timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndipo timathandizira kuyeretsa dzina lake. (Sal. 83:18; Ezek. 36:23; Mat. 6:9) Mofanana ndi mmene Yesu anachitira pa utumiki wake, ifenso tikamachita utumiki nthawi zonse timasonyeza kuti timafuna ndi mtima wonse kuti dzina la Yehova liyeretsedwe komanso kuti chifuniro chake chichitike.—Mat. 26:39.

3. Kodi kukonda Yehova kumatithandiza bwanji kuthana ndi mavuto?

3 Chikondi Chimatipangitsa Kuthana ndi Mavuto: Kukonda Yehova kungatithandize kuthana ndi mavuto aliwonse amene tingakumane nawo mu utumiki. (1 Akor. 13:4, 7) Yesu anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake amene akanam’pangitsa kusiya utumiki wake. Komabe, anathana nawo chifukwa chakuti ankakonda kwambiri Yehova komanso ankafunitsitsa kuchita chifuniro Chake. (Maliko 3:21; 1 Pet. 2:18-23) Ifenso timakumana ndi mavuto ambiri, ndipo kukonda Mulungu n’kumene kungatithandize kuti tithane nawo. Tikamatsatira kwambiri chitsanzo cha Khristu, tingakhale olimba mtima ndiponso opanda mantha pokwaniritsa utumiki wathu. N’zoona kuti tingakumane ndi mavuto monga kutsutsidwa ndi achibale, kudwala, ukalamba ndi tsankho. Komabe, zimenezi sizimatilepheretsa kusonyeza kuti timakonda Yehova mwa kuyesetsa kuchita utumiki wathu mogwira mtima.

4. Kodi kukonda Yehova kumatipatsa mwayi wotani?

4 Chikondi n’champhamvu, ndipo ndife odala kuti tingathe kusonyeza kuti timakonda Mulungu ndi moyo wathu wonse tikamachita utumiki. (1 Akor. 13:13) Pamene tikuyandikira kwambiri nthawi imene dzina la Yehova lidzayeretsedweratu, ‘chikondi chathu chipitirizetu kukula.’—Afil. 1:9; Mat. 22:36-38.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena